2 M’masiku otsiriza,+ phiri la nyumba+ ya Yehova lidzakhazikika pamwamba pa nsonga za mapiri,+ ndipo lidzakwezedwa pamwamba pa mapiri ang’onoang’ono.+ Mitundu yonse idzakhamukira kumeneko.+
10 M’tsiku limenelo,+ padzakhala muzu wa Jese+ womwe udzaimirire ngati chizindikiro kwa anthu.+ Ngakhale anthu a mitundu ina adzatembenukira kwa iye kuti awatsogolere,+ ndipo malo ake okhalapo adzakhala aulemerero.+
11 Koma ndikukutsimikizirani kuti ambiri ochokera kum’mawa ndi kumadzulo+ adzabwera ndi kukhala patebulo limodzi ndi Abulahamu, Isaki ndi Yakobo mu ufumu+ wakumwamba,+