Ezekieli 38:21 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 21 “‘Ndidzamubweretsera lupanga m’madera anga onse a m’mapiri kuti limuwononge,’ watero Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa.+ ‘Aliyense adzapha m’bale wake ndi lupanga.+ Mika 7:2 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 2 Anthu okhulupirika atha padziko lapansi, ndipo pakati pa anthu palibe munthu wowongoka mtima.+ Onse amadikirira anzawo kuti akhetse magazi.+ Aliyense amasaka m’bale wake ndi ukonde.+ Hagai 2:22 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 22 Ndithu ndidzagonjetsa maufumu ndi kuchotsa mphamvu za maufumu a anthu a mitundu ina.+ Ndiwononga magaleta* ndi okwera pamagaletawo. Mahatchi* ndi okwera mahatchiwo adzaphedwa.+ Aliyense adzapha m’bale wake ndi lupanga.’”+ Zekariya 11:9 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 9 Pambuyo pake ndinanena kuti: “Ndileka kukuwetani.+ Amene akufa, afe.+ Amene akuwonongeka, awonongeke. Otsalawo adyane.”+ Zekariya 14:13 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 13 “Pa tsiku limenelo Yehova adzawasokoneza kwambiri.+ Aliyense adzagwira dzanja la mnzake, ndipo aliyense adzamenya mnzake ndi dzanja lake.
21 “‘Ndidzamubweretsera lupanga m’madera anga onse a m’mapiri kuti limuwononge,’ watero Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa.+ ‘Aliyense adzapha m’bale wake ndi lupanga.+
2 Anthu okhulupirika atha padziko lapansi, ndipo pakati pa anthu palibe munthu wowongoka mtima.+ Onse amadikirira anzawo kuti akhetse magazi.+ Aliyense amasaka m’bale wake ndi ukonde.+
22 Ndithu ndidzagonjetsa maufumu ndi kuchotsa mphamvu za maufumu a anthu a mitundu ina.+ Ndiwononga magaleta* ndi okwera pamagaletawo. Mahatchi* ndi okwera mahatchiwo adzaphedwa.+ Aliyense adzapha m’bale wake ndi lupanga.’”+
9 Pambuyo pake ndinanena kuti: “Ndileka kukuwetani.+ Amene akufa, afe.+ Amene akuwonongeka, awonongeke. Otsalawo adyane.”+
13 “Pa tsiku limenelo Yehova adzawasokoneza kwambiri.+ Aliyense adzagwira dzanja la mnzake, ndipo aliyense adzamenya mnzake ndi dzanja lake.