Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • 2 Mafumu 24:15
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 15 Chotero iye anatengera Yehoyakini+ ku Babulo.+ Anatenga ku Yerusalemu mayi a mfumuyo,+ akazi ake, nduna za panyumba yake,+ ndi akuluakulu a m’dzikolo, n’kuwapititsa ku Babulo.

  • 2 Mbiri 36:10
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 10 Kumayambiriro+ kwa chaka, Mfumu Nebukadinezara inatuma+ asilikali ake omwe anakamutenga n’kubwera naye ku Babulo+ limodzi ndi zinthu zabwinozabwino za m’nyumba ya Yehova.+ Kuwonjezera apo, Nebukadinezara analonga ufumu Zedekiya+ yemwe anali m’bale wa bambo ake kukhala mfumu ya Yuda ndi Yerusalemu.+

  • Yeremiya 27:20
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 20 zimene Nebukadinezara mfumu ya Babulo anasiya pamene anatenga Yekoniya+ mwana wa Yehoyakimu, mfumu ya Yuda, pamodzi ndi olemekezeka onse a Yuda ndi Yerusalemu, kupita nawo ku ukapolo ku Babulo kuchokera ku Yerusalemu.+

  • Yeremiya 29:2
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 2 Pamene analemba kalata imeneyi, mfumu Yekoniya,+ mayi a mfumu,+ nduna za panyumba ya mfumu, akalonga a Yuda ndi Yerusalemu,+ amisiri ndi omanga makoma achitetezo+ anali atatengedwa kupita ku ukapolo kuchokera ku Yerusalemu.

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena