113 Tamandani Ya, anthu inu!+
Inu atumiki a Yehova, mutamandeni,+
Tamandani dzina la Yehova.+
2 Dzina la Yehova lidalitsike,+
Kuyambira tsopano mpaka kalekale.+
3 Kuyambira kotulukira dzuwa mpaka kumene limalowera,+
Dzina la Yehova liyenera kutamandidwa.+
4 Yehova wakwezeka pamwamba pa mitundu yonse ya anthu.+
Ulemerero wake uli pamwamba pa kumwamba.+
5 Ndani angafanane ndi Yehova Mulungu wathu,+
Amene amakhala pamwamba?+
6 Iye amatsika m’munsi kuti aone kumwamba ndi dziko lapansi.+
7 Amadzutsa munthu wonyozeka kumuchotsa m’fumbi.+
Amakweza munthu wosauka kumuchotsa padzala,+
8 Kuti amukhazike pamodzi ndi anthu olemekezeka,+
Pamodzi ndi anthu olemekezeka pakati pa anthu a Mulungu.+
9 Akuchititsa mkazi wosabereka kukhala m’nyumba+
Monga mayi wosangalala wa ana aamuna.+
Tamandani Ya, anthu inu!+