Numeri 6:3 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 3 azisala vinyo ndi zakumwa zina zoledzeretsa.+ Asamamwe ngakhale viniga* wochokera ku vinyo, kapena viniga wochokera ku zakumwa zina zoledzeretsa, kapenanso madzi a mphesa. Ndiponso asamadye mphesa zaziwisi kapena zouma. Oweruza 13:4 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 4 Choncho samala, usamwe vinyo kapena chakumwa chilichonse choledzeretsa,+ ndipo usadye chilichonse chodetsedwa.+ Mateyu 3:4 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 4 Koma Yohane ameneyu, anali kuvala chovala chaubweya wa ngamila+ ndi lamba wachikopa+ m’chiuno mwake. Chakudya chake chinali dzombe+ ndi uchi.+ Maliko 1:6 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 6 Yohane ameneyu anali kuvala chovala cha ubweya wa ngamila ndi lamba wachikopa m’chiuno mwake,+ ndipo anali kudya dzombe+ ndi uchi.+ Luka 1:15 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 15 chifukwa adzakhala wamkulu pamaso pa Yehova.+ Koma asadzamwe vinyo ngakhale pang’ono+ kapena chakumwa chaukali chilichonse. Ndipo adzadzazidwa ndi mzimu woyera kuyambira ali m’mimba mwa mayi ake.+
3 azisala vinyo ndi zakumwa zina zoledzeretsa.+ Asamamwe ngakhale viniga* wochokera ku vinyo, kapena viniga wochokera ku zakumwa zina zoledzeretsa, kapenanso madzi a mphesa. Ndiponso asamadye mphesa zaziwisi kapena zouma.
4 Choncho samala, usamwe vinyo kapena chakumwa chilichonse choledzeretsa,+ ndipo usadye chilichonse chodetsedwa.+
4 Koma Yohane ameneyu, anali kuvala chovala chaubweya wa ngamila+ ndi lamba wachikopa+ m’chiuno mwake. Chakudya chake chinali dzombe+ ndi uchi.+
6 Yohane ameneyu anali kuvala chovala cha ubweya wa ngamila ndi lamba wachikopa m’chiuno mwake,+ ndipo anali kudya dzombe+ ndi uchi.+
15 chifukwa adzakhala wamkulu pamaso pa Yehova.+ Koma asadzamwe vinyo ngakhale pang’ono+ kapena chakumwa chaukali chilichonse. Ndipo adzadzazidwa ndi mzimu woyera kuyambira ali m’mimba mwa mayi ake.+