13 ‘Ndikudziwa kumene ukukhala. Ukukhala kumene kuli mpando wachifumu wa Satana. Koma ukugwirabe mwamphamvu dzina langa,+ ndipo sunakane kuti umakhulupirira ine.+ Sunakane ngakhale m’masiku a Antipa mboni yanga,+ wokhulupirika wanga uja, amene anaphedwa+ pambali panu, kumene Satana akukhala.