Nkhani za M’baibulo Zokambirana
1. Aneneri Onyenga
A. Ananeneratu za aneneri onyenga, analiko m’masiku a atumwi
Njira yodziwira aneneri onyenga. De 18:20-22; Lu 6:26
Ananeneratu za iwo, amadziwika ndi zipatso zawo. Mt 24:23-26; 7:15-23
2. Aramagedo
A. Nkhondo ya Mulungu yothetsa zoipa zonse
Mitundu idzasonkhanitsidwa pa Aramagedo. Chv 16:14, 16
Mulungu adzamenya nkhondoyo, pogwiritsa ntchito Mwana wake ndi angelo. 2At 1:6-9; Chv 19:11-16
Mmene tingadzapulumukire. Zef 2:2, 3; Chv 7:14
B. Sikulephera kwa chikondi cha Mulungu
Dziko laipa kwambiri. 2Ti 3:1-5
Mulungu wakhala woleza mtima, koma ayenera kuchitapo kanthu chifukwa cha chilungamo. 2Pe 3:9, 15; Lu 18:7, 8
Oipa ayenera kuchoka kuti olungama asangalale. Miy 21:18; Chv 11:18
3. Baibulo
A. Mawu a Mulungu ndi ouziridwa
Anthu anatsogoleredwa ndi mzimu wa Mulungu kuti alembe. 2Pe 1:20, 21
Muli ulosi: Da 8:5, 6, 20-22; Lu 21:5, 6, 20-22; Yes 45:1-4
Baibulo lonse ndi louziridwa ndipo n’lopindulitsa. 2Ti 3:16, 17; Aro 15:4
B. Limapereka malangizo othandiza m’masiku athu ano
Kunyalanyaza mfundo za m’Baibulo n’kotayitsa moyo. Aro 1:28-32
Nzeru za anthu sizingalowe m’malo mwake. 1Ak 1:21, 25; 1Ti 6:20
N’chitetezo kwa mdani wamphamvu koposa. Aef 6:11, 12, 17
Limatsogolera anthu m’njira yoyenera. Sl 119:105; 2Pe 1:19; Miy 3:5, 6
C. Linalembedwera anthu a mitundu yonse ndi a mafuko onse
Baibulo linayamba kulembedwa kumayiko a Kum’mawa. Eks 17:14; 24:12, 16; 34:27
Mphatso ya Mulungu imeneyi si ya Azungu okha. Aro 10:11-13; Aga 3:28
Mulungu amalandira anthu, kaya akhale otani. Mac 10:34, 35; Aro 5:18; Chv 7:9, 10
4. Chikumbutso, Misa
A. Kuchita chikumbutso cha Chakudya Chamadzulo cha Ambuye
Kumachitika kamodzi pa chaka, pa deti la Pasika. Lu 22:1, 17-20; Eks 12:14
Ndi kukumbukira imfa ya Khristu yopereka nsembe. 1Ak 11:26; Mt 26:28
Amene ali ndi chiyembekezo chopita kumwamba amadya mkate ndi kumwa vinyo. Lu 22:29, 30; 12:32, 37
Mmene munthu amadziwira kuti ali ndi chiyembekezo chimenecho. Aro 8:15-17
B. Misa si ya m’Malemba
Kuti machimo akhululukidwe, pamafunika pakhetsedwe magazi. Ahe 9:22
Khristu ndiye Mkhalapakati yekhayo wa pangano latsopano. 1Ti 2:5, 6; Yoh 14:6
Khristu ali kumwamba, satsitsidwa pansi ndi wansembe. Mac 3:20, 21
Kubwereza nsembe ya Khristu n’kosafunikira. Ahe 9:24-26; 10:11-14
5. Chilengedwe
A. Chimagwirizana ndi sayansi yokhala ndi umboni wodalirika, chimatsutsa zoti zamoyo zinachita kusandulika
Sayansi imagwirizana ndi ndondomeko ya kulengedwa kwa zinthu. Ge 1:11, 12, 21, 24, 25
Lamulo la Mulungu lokhudza “mitundu” ya zolengedwa ndi loona. Ge 1:11, 12; Yak 3:12
B. Masiku olenga zinthu sanali masiku a maola 24
“Tsiku” lingatanthauze nthawi ya masiku ambiri. Ge 2:4
Kwa Mulungu, tsiku lingakhale nthawi yaitali. Sl 90:4; 2Pe 3:8
6. Chipembedzo
A. Chipembedzo choona n’chimodzi chokha
Chiyembekezo chimodzi, chikhulupiriro chimodzi, ubatizo umodzi. Aef 4:5, 13
Chinapatsidwa ntchito yophunzitsa anthu kuti akhale ophunzira. Mt 28:19; Mac 8:12; 14:21
Chimadziwika ndi zipatso zake. Mt 7:19, 20; Lu 6:43, 44; Yoh 15:8
Chikondi, anthu ake amalankhula zofanana. Yoh 13:35; 1Ak 1:10; 1Yoh 4:20
B. Sikulakwa kutsutsa ziphunzitso zonama
Yesu anatsutsa ziphunzitso zonama. Mt 23:15, 23, 24; 15:4-9
Anatero kuti ateteze amene anachititsidwa khungu. Mt 15:14
Choonadi chinawamasula kuti akhale ophunzira a Yesu. Yoh 8:31, 32
C. M’pofunika kusintha chipembedzo chako chikapezeka kuti n’cholakwika
Choonadi chimamasula, chimaonetsa kuti ambiri ndi olakwa. Yoh 8:31, 32
Aisiraeli ndi enanso, anasiya chipembedzo chawo chakale. Yos 24:15; 2Mf 5:17
Akhristu oyambirira anasintha maganizo awo. Aga 1:13, 14; Mac 3:17, 19
Paulo anasintha chipembedzo chake. Mac 26:4-6
Dziko lonse lanyengedwa, liyenera kusintha maganizo. Chv 12:9; Aro 12:2
D. Zooneka ngati “zabwino m’zipembedzo zonse” si zimene Mulungu amavomerezera chipembedzo
Mulungu ndiye amanena mmene tiyenera kumulambirira. Yoh 4:23, 24; Yak 1:27
Si zabwino ngati n’zosagwirizana ndi chifuniro cha Mulungu. Aro 10:2, 3
“Ntchito zabwino” zitha kukanidwa. Mt 7:21-23
Chimadziwika ndi zipatso zake. Mt 7:20
7. Chipulumutso
A. Chipulumutso chimachokera kwa Mulungu kudzera mu nsembe ya Yesu ya dipo
Moyo ndi mphatso ya Mulungu kudzera mwa Mwana wake. 1Yoh 4:9, 14; Aro 6:23
Chipulumutso n’chotheka kudzera mu nsembe ya Yesu yokha basi. Mac 4:12
Kulapa pomwalira sikukhala ndi ntchito za kulapa. Yak 2:14, 26
Tiyenera kuyesetsa mwamphamvu kuti tichipeze. Lu 13:23, 24; 1Ti 4:10
B. Mfundo yakuti “ukapulumutsidwa, wapulumutsidwa basi” si ya m’Malemba
Amene amalandira nawo mzimu woyera akhoza kugwa mwauzimu. Ahe 6:4, 6; 1Ak 9:27
Aisiraeli ambiri anawonongedwa ngakhale kuti anali atapulumutsidwa ku Iguputo. Yuda 5
Chipulumutso sichibwera kamodzi n’kamodzi. Afi 2:12; 3:12-14; Mt 10:22
Obwerera m’mbuyo amakhala oipa kwambiri kuposa poyamba. 2Pe 2:20, 21
C. Chiphunzitso chakuti “aliyense adzapulumuka” si cha m’Malemba
Ena sangathe kulapa. Ahe 6:4-6
Mulungu sakondwera ndi imfa ya oipa. Eze 33:11; 18:32
Koma chikondi sichilekerera zosalungama. Ahe 1:9
Oipa adzawonongedwa. Ahe 10:26-29; Chv 20:7-15
8. Dipo
A. Moyo wa Yesu pamene anali munthu unaperekedwa monga “dipo la onse”
Yesu anapereka moyo wake dipo. Mt 20:28
Magazi ake amtengo wapatali amafafaniza machimo. Ahe 9:14, 22
Nsembe imodzi ndi yokwanira mpaka kalekale. Aro 6:10; Ahe 9:26
Munthu ayenera kuchitapo kanthu kuti apindule nayo, ayenera kuvomereza nsembeyo. Yoh 3:16
B. Dipolo linali lofanana ndi zimene zinatayika
Adamu analengedwa wangwiro. De 32:4; Mla 7:29; Ge 1:31
Atachimwa, anakhala wopanda ungwiro ndipo anachititsanso kuti ana ake akhale opanda ungwiro. Aro 5:12, 18
Ana sakanatha kuchitapo kanthu, panafunikira wofanana ndendende ndi Adamu. Sl 49:7; De 19:21
Moyo wangwiro wa Yesu pamene anali munthu unaperekedwa kuti ukhale dipo. 1Ti 2:5, 6; 1Pe 1:18, 19
9. Dziko Lapansi
A. Cholinga cha Mulungu chokhudza dziko lapansi
Paradaiso anapangidwa padziko lapansi kuti anthu angwiro akhalemo. Ge 1:28; 2:8-15
Cholinga cha Mulungu chidzakwaniritsidwa. Yes 55:11; 46:10, 11
Dziko lidzadzaza ndi anthu angwiro amtendere. Sl 72:7; Yes 45:18; 9:6, 7
Ufumu udzabwezeretsa Paradaiso. Mt 6:9, 10; Chv 21:3-5
B. Silidzawonongedwa kapena kukhala lopanda anthu
Dziko lapansi lenilenili lidzakhalapo mpaka kalekale. Mla 1:4; Sl 104:5
Mu nthawi ya Nowa anthu ndiwo anawonongedwa, osati dziko lapansi. 2Pe 3:5-7; Ge 7:23
Chitsanzochi chikutipatsa chiyembekezo chakuti anthu apulumuka mu nthawi yathu ino. Mt 24:37-39
Oipa adzawonongedwa, “khamu lalikulu” lidzapulumuka. 2At 1:6-9; Chv 7:9, 14
10. Imfa
A. Chochititsa imfa
Pa chiyambi anthu anali angwiro, anali ndi chiyembekezo chokhala ndi moyo wosatha. Ge 1:28, 31
Kusamvera kunabweretsa chiweruzo cha imfa. Ge 2:16, 17; 3:17, 19
Uchimo ndi imfa zinafikanso kwa ana onse a Adamu. Aro 5:12
B. Mmene akufa alili
Akufa sazindikira kanthu, sadziwa chilichonse. Mla 9:5, 10; Sl 146:3, 4
Akufa ali m’tulo kuyembekezera kuukitsidwa. Yoh 11:11-14, 23-26; Mac 7:60
C. N’zosatheka kulankhula ndi akufa
Akufa sali ndi moyo limodzi ndi Mulungu monga mizimu. Sl 115:17; Yes 38:18
Tikuchenjezedwa kuti tisayese kulankhula ndi akufa. Yes 8:19; Le 19:31
Olankhula ndi mizimu, olosera za m’tsogolo, n’ngosavomerezedwa. De 18:10-12; Aga 5:19-21
11. Kubweranso kwa Khristu
A. Kubweranso kwake n’kosaoneka kwa anthu
Anauza ophunzira ake kuti dziko silidzamuonanso. Yoh 14:19
Ophunzira okha ndiwo anamuona akukwera kumwamba, chimodzimodzi pa kubweranso kwake. Mac 1:6, 10, 11
Ali kumwamba monga mzimu wosaoneka. 1Ti 6:14-16; Ahe 1:3
Abwerera monga mfumu yamphamvu ya Ufumu wakumwamba. Da 7:13, 14
B. Kudzadziwika ndi zochitika zooneka ndi maso
Ophunzira anapempha chizindikiro cha kukhalapo kwake. Mt 24:3
Akhristu “amaona” kukhalapo kwake mwa kuzindikira zochitika. Aef 1:18
Zochitika zambiri zikusonyeza umboni wa kukhalapo kwake. Lu 21:10, 11
Adani “adzaona” chiwonongeko chitawagwera. Chv 1:7
12. Kuchiritsa, Malilime
A. Kuchiritsidwa mwauzimu kumapindulitsa kwamuyaya
Matenda auzimu amawononga. Yes 1:4-6; 6:10; Ho 4:6
Kuchiritsa kwauzimu ndiko ntchito yaikulu imene tapatsidwa. Yoh 6:63; Lu 4:18
Kumachotsa machimo, kumapereka chimwemwe ndi moyo. Yak 5:19, 20; Chv 7:14-17
B. Mu Ufumu wa Mulungu anthu adzachiritsidwa ndipo sadzadwalanso
Yesu anachiritsa matenda, analalikira za madalitso a Ufumu. Mt 4:23
Ufumu wolonjezedwawo ndiwo njira yokhayo yochiritsira anthu kuti asadzadwalenso. Mt 6:10; Yes 9:7
Ngakhale imfa idzathetsedwa. 1Ak 15:25, 26; Chv 21:4; 20:14
C. Kuchiritsa kwamasiku ano kulibe umboni wakuti Mulungu amakuvomereza
Ophunzira sanali kudzichiritsa okha mozizwitsa. 2Ak 12:7-9; 1Ti 5:23
Mphatso zozizwitsa zinapita ndi masiku a atumwi. 1Ak 13:8-11
Kuchiritsa si umboni wotsimikizira kuti munthu akuvomerezedwa ndi Mulungu. Mt 7:22, 23; 2At 2:9-11
D. Kulankhula malilime kunali dongosolo lakanthawi chabe
Kunali chizindikiro, anthuwo anayenera kuyesetsa kupeza mphatso zina zazikulu. 1Ak 14:22; 12:30, 31
Ananeneratu kuti mphatso zozizwitsa za mzimu zidzatha. 1Ak 13:8-10
Kuchita zinthu zodabwitsa si umboni wotsimikizira kuti munthu akuvomerezedwa ndi Mulungu. Mt 7:22, 23; 24:24
13. Kuchitira Umboni
A. Akhristu onse ayenera kuchitira umboni, kuuza ena uthenga wabwino
Ayenera kuvomereza Yesu pamaso pa anthu kuti iwonso avomerezedwe. Mt 10:32
Ayenera kuchita zimene Mawu amanena, posonyeza chikhulupiriro. Yak 1:22-24; 2:24
Atsopano nawonso ayenera kukhala aphunzitsi. Mt 28:19, 20
Kulengeza pamaso pa anthu kumabweretsa chipulumutso. Aro 10:10
B. Kufunika kwa kufikira anthu mobwerezabwereza, kupitirizabe kulalikira
Chenjezo la mapeto liyenera kuperekedwa. Mt 24:14
Yeremiya analengeza kwa zaka zambiri mapeto a Yerusalemu. Yer 25:3
Mofanana ndi Akhristu oyambirira, sitingaleke. Mac 4:18-20; 5:28, 29
C. Tiyenera kuchitira umboni kuti tisakhale ndi mlandu wa magazi
Tiyenera kuchenjeza za mapeto amene akuyandikira. Eze 33:7; Mt 24:14
Kulephera kutero kumabweretsa mlandu wa magazi. Eze 33:8, 9; 3:18, 19
Paulo analibe mlandu wa magazi, analankhula choonadi chonse. Mac 20:26, 27; 1Ak 9:16
Kumapulumutsa wochitira umboniyo ndi womvetserayo. 1Ti 4:16; 1Ak 9:22
14. Kulambira Makolo Akale
A. Kulambira makolo akale n’kosathandiza
Makolo akale n’ngakufa, sadziwa kalikonse. Mla 9:5, 10
Makolo oyambirira ndi osayenera kuwalambira. Aro 5:12, 14; 1Ti 2:14
Mulungu amaletsa kulambira koteroko. Eks 34:14; Mt 4:10
B. Anthu angalemekezedwe, koma Mulungu yekha ndiye ayenera kulambiridwa
Achinyamata ayenera kulemekeza achikulire. 1Ti 5:1, 2, 17; Aef 6:1-3
Koma Mulungu yekha ndiye woyenera kumulambira. Mac 10:25, 26; Chv 22:8, 9
15. Kulambira Mariya
A. Mariya anali amayi a Yesu, osati “amayi a Mulungu”
Mulungu alibe chiyambi. Sl 90:2; 1Ti 1:17
Mariya anali amayi a Mwana wa Mulungu, pamene anali padziko lapansi. Lu 1:35
B. Mariya sanali “namwali moyo wake wonse”
Anakwatiwa ndi Yosefe. Mt 1:19, 20, 24, 25
Anakhalanso ndi ana ena kuwonjezera pa Yesu. Mt 13:55, 56; Lu 8:19-21
Pa nthawiyo iwo sanali ‘abale ake auzimu.’ Yoh 7:3, 5
16. Kumwamba
A. Anthu 144,000 okha ndiwo adzapite kumwamba
N’chiwerengero chochepa chabe, adzakhala mafumu limodzi ndi Khristu. Chv 5:9, 10; 20:4
Yesu anali kalambulabwalo, enanso anasankhidwa kuyambira nthawiyo. Akl 1:18; 1Pe 2:21
Anthu ena ambiri adzakhala padziko lapansi. Sl 72:8; Chv 21:3, 4
A 144,000 ali ndi udindo wapadera, palibenso ena ali nawo. Chv 14:1, 3; 7:4, 9
17. Kuphatikiza Zipembedzo
A. Kuphatikiza zipembedzo si kovomerezeka ndi Mulungu
Pali njira imodzi yokha, yopanikiza, oipeza ndi owerengeka. Aef 4:4-6; Mt 7:13, 14
Timachenjezedwa kuti ziphunzitso zonama zingatiipitse. Mt 16:6, 12; Aga 5:9
Tikulamulidwa kukhala olekana ndi enawo. 2Ti 3:5; 2Ak 6:14-17; Chv 18:4
B. Mfundo yakuti muli “zabwino m’zipembedzo zonse” si yoona
Ena ndi odzipereka koma mosagwirizana ndi Mulungu. Aro 10:2, 3
Choipa chimawononga zimene zikanakhala zabwino. 1Ak 5:6; Mt 7:15-17
Aphunzitsi onyenga ndi ophetsa. 2Pe 2:1; Mt 12:30; 15:14
Kulambira koyera kumafuna kuti munthu akhale wodzipereka ndi mtima wonse. De 6:5, 14, 15
18. Kutsutsidwa, Kuzunzidwa
A. Chifukwa chimene Akhristu amatsutsidwira
Yesu anadedwa, ananeneratu kuti Akhristu adzatsutsidwa. Yoh 15:18-20; Mt 10:22
Kutsatira mfundo zoyenera kumatsutsa dziko. 1Pe 4:1, 4, 12, 13
Satana, mulungu wa nthawi ino, amatsutsa Ufumu. 2Ak 4:4; 1Pe 5:8
Mkhristu saopa, Mulungu amathandiza. Aro 8:38, 39; Yak 4:8
B. Mkazi asalole kuti mwamuna wake amulekanitse ndi Mulungu
Akuchenjezedwa kuti anthu ena angauze mwamuna wake zolakwika. Mt 10:34-38; Mac 28:22
Mkazi adalire Mulungu ndi Khristu. Yoh 6:68; 17:3
Kukhulupirika kwake kungapulumutsenso mwamuna wake. 1Ak 7:16; 1Pe 3:1-6
Mwamuna ndiye mutu, koma asalamule pa nkhani ya kulambira. 1Ak 11:3; Mac 5:29
C. Mwamuna asalole kuti mkazi wake amuletse kutumikira Mulungu
Akonde mkazi wake ndi banja lake, azifuna kuti iwo adzapeze moyo. 1Ak 7:16
Ali ndi udindo wosankhira banja lake zochita ndi kulipezera zosowa. 1Ak 11:3; 1Ti 5:8
Mulungu amakonda mwamuna wokhala ku mbali ya choonadi. Yak 1:12; 5:10, 11
Kugonjera potsutsidwa n’cholinga chakuti pakhale mtendere kumachititsa kuti Mulungu asakukonde. Ahe 10:38
Ayenera kutsogolera banja lake kuti lidzapeze moyo wosangalala m’dziko latsopano. Chv 21:3, 4
19. Kuuka kwa Akufa
A. Chiyembekezo chokhudza akufa
Onse amene ali m’manda adzaukitsidwa. Yoh 5:28, 29
Kuukitsidwa kwa Yesu kumatsimikizira zimenezi. 1Ak 15:20-22; Mac 17:31
Ochimwira mzimu sadzauka. Mt 12:31, 32
Okhulupirira akutsimikiziridwa kuti adzauka. Yoh 11:25
B. Kuukitsidwira ku moyo wakumwamba kapena padziko lapansi
Onse amafa mwa Adamu, amalandira moyo mwa Yesu. 1Ak 15:20-22; Aro 5:19
Amaukitsidwa ndi matupi osiyanasiyana. 1Ak 15:40, 42, 44
Okhala ndi Yesu adzakhala ngati iyeyo. 1Ak 15:49; Afi 3:20, 21
Osakhala ndi udindo wolamulira adzakhala padziko lapansi. Chv 20:4b, 5, 13; 21:3, 4
20. Kuwerengera Nthawi
A. Nthawi za Akunja zinatha mu 1914 (C.E.)
Mzere wa mafumu olamulira unadulidwa mu 607 B.C.E. Eze 21:25-27
Panayenera kudutsa “Nthawi 7” kuti ulamulirowo aubwezeretse. Da 4:32, 16, 17
Nthawi 7 = nthawi 3 1⁄2 × 2, kapena masiku 1,260 × 2. Chv 12:6, 14; 11:2, 3
Tsiku limodzi kuimira chaka chimodzi. [Zikukwana zaka 2,520] Eze 4:6; Nu 14:34
Zakazo zinadzafika mpaka pa kukhazikitsidwa kwa Ufumu. Lu 21:24; Da 7:13, 14
21. Magazi
A. Kuikidwa magazi n’kusalemekeza kupatulika kwa magazi
Nowa anauzidwa kuti magazi ndi opatulika, ndiwo moyowo. Ge 9:4, 16
Pangano la Chilamulo linaletsa kudya magazi. Le 17:14; 7:26, 27
Akhristu anapatsidwanso lamulo limenelo. Mac 15:28, 29; 21:25
B. Kupulumutsa moyo si chifukwa chophwanyira lamulo la Mulungu
Kumvera kuposa nsembe. 1Sa 15:22; Mko 12:33
Kuika moyo wako patsogolo pa lamulo la Mulungu n’kophetsa. Mko 8:35, 36
22. Maholide, Masiku a Kubadwa
A. Akhristu oyambirira sanali kusunga masiku a kubadwa, Khirisimasi
Amene si olambira oona ndiwo anasunga masikuwo. Ge 40:20; Mt 14:6
Tsiku la imfa ya Yesu liyenera kukumbukiridwa. Lu 22:19, 20; 1Ak 11:25, 26
Kuchita maphwando a phokoso pa tsikulo n’kosayenera. Aro 13:13; Aga 5:21; 1Pe 4:3
23. Masiku Otsiriza
A. Kodi “mapeto a dziko” amatanthauzanji?
Kutha kwa nthawi ino. Mt 24:3; 2Pe 3:5-7; Mko 13:4
Si kutha kwa dziko lapansi, koma kwa nthawi yoipa ino. 1Yoh 2:17
Nthawi ya mapeto choyamba, kenako chiwonongeko. Mt 24:14
Kupulumuka kwa olungama, kenako dziko latsopano. 2Pe 2:9; Chv 7:14-17
B. Kufunika kokhala maso n’kumaona zizindikiro za masiku otsiriza
Zizindikiro zinaperekedwa ndi Mulungu kuti zititsogolere. 2Ti 3:1-5; 1At 5:1-4
Dziko silizindikira kuopsa kwake. 2Pe 3:3, 4, 7; Mt 24:39
Mulungu sakuchedwa, koma akupereka chenjezo. 2Pe 3:9
Mphoto ya kukhala maso, osamala. Lu 21:34-36
24. Mboni za Yehova
A. Chiyambi cha Mboni za Yehova
Yehova amadziwikitsa mboni zake. Yes 43:10-12; Yer 15:16
Mzera wa mboni zokhulupirika unayambira pa Abele. Ahe 11:4, 39; 12:1
Yesu anali mboni yokhulupirika ndi yoona. Yoh 18:37; Chv 1:5; 3:14
25. Mdyerekezi, Ziwanda
A. Mdyerekezi ndi munthu wauzimu
Si zoipa za mumtima wa munthu koma iye ndi munthu wauzimu. 2Ti 2:26
Mdyerekezi ndi munthu wauzimu monga alili angelo. Mt 4:1, 11; Yob 1:6
Anadzipanga yekha kukhala Mdyerekezi polakalaka zinthu zoipa. Yak 1:13-15
B. Mdyerekezi ndiye wolamulira wosaoneka wa dziko
Dziko likulamulidwa ndi iye monga mulungu wake. 2Ak 4:4; 1Yoh 5:19; Chv 12:9
Analoledwa kukhalapobe mpaka nkhani idzathetsedwe. Eks 9:16; Yoh 12:31
Adzaponyedwa m’phompho, kenako adzawonongedwa. Chv 20:2, 3, 10
C. Ziwanda ndi angelo opanduka
Zinagwirizana ndi Satana Chigumula chisanachitike. Ge 6:1, 2; 1Pe 3:19, 20
Zinatsitsidwa, sizilandiranso kuunika kulikonse. 2Pe 2:4; Yuda 6
Zimalimbana ndi Mulungu, zimapondereza anthu. Lu 8:27-29; Chv 16:13, 14
Zidzawonongedwa pamodzi ndi Satana. Mt 25:41; Lu 8:31; Chv 20:2, 3, 10
26. Moto
A. Moto ukuphiphiritsira chiwonongeko
Moto ukuphiphiritsira kuwonongedwa mwa kuphedwa. Mt 25:41, 46; 13:30
Anthu oipa osalapa adzawonongedweratu ngati mmene moto umawonongera. Ahe 10:26, 27
‘Kuzunzidwa’ kwa Satana m’moto ndiko imfa yosabwererako. Chv 20:10, 14, 15
B. Nkhani ya munthu wachuma ndi Lazaro si umboni wakuti anthu adzazunzidwa kwamuyaya
Motowo ndi wophiphiritsa monganso kukhala pachifuwa cha Abulahamu. Lu 16:22-24
Kuvomerezedwa ndi Abulahamu anakusiyanitsanso ndi mdima. Mt 8:11, 12
Kuwonongedwa kwa Babulo kumatchedwanso kuzunzidwa m’moto. Chv 18:8-10, 21
27. Moyo
A. Anthu omvera akutsimikiziridwa kuti adzapeza moyo wosatha
Mulungu, amene sanganame, analonjeza moyo. Tit 1:2; Yoh 10:27, 28
Okhulupirira akutsimikiziridwa kuti adzapeza moyo wamuyaya. Yoh 11:25, 26
Imfa idzawonongedwa. 1Ak 15:26; Chv 21:4; 20:14; Yes 25:8
B. Moyo wakumwamba ndi wa okhawo amene ali m’thupi la Khristu
Mulungu amasankha anthu amene iye wafuna. Mt 20:23; 1Ak 12:18
Anthu 144,000 okha osankhidwa padziko lapansi. Chv 14:1, 4; 7:2-4; 5:9, 10
Ngakhale Yohane M’batizi sadzakhala mu Ufumu wakumwamba. Mt 11:11
C. Moyo wa padziko lapansi unalonjezedwa kwa anthu osawerengeka, “nkhosa zina”
Ochepa chabe ndiwo adzakhale ndi Yesu kumwamba. Chv 14:1, 4; 7:2-4
“Nkhosa zina” si abale a Khristu. Yoh 10:16; Mt 25:32, 40
Ambiri akusonkhanitsidwa panopa kuti adzapulumuke padziko lapansi. Chv 7:9, 15-17
Ena adzaukitsidwa kuti akhale ndi moyo padziko lapansi. Chv 20:12; 21:4
28. Mtanda
A. Yesu anapachikidwa pamtengo wopherapo olakwa kuti anyozeke
Yesu anapachikidwa pamtengo wopherapo anthu olakwa. Mac 5:30; 10:39; Aga 3:13
Akhristu ayenera kunyamula mtengowo, kutanthauza kuti ayenera kunyozeka. Mt 10:38; Lu 9:23
B. Suyenera kulambiridwa
Kuonetsera mtengo umene Yesu anaferapo ndi mnyozo. Ahe 6:6; Mt 27:41, 42
Kugwiritsa ntchito mtanda polambira ndi kulambira mafano. Eks 20:4, 5; Yer 10:3-5
Yesu ndi mzimu, salinso pamtengo. 1Ti 3:16; 1Pe 3:18
29. Mtumiki
A. Akhristu onse ayenera kukhala atumiki
Yesu anali mtumiki wa Mulungu. Aro 15:8, 9; Mt 20:28
Akhristu amatsatira chitsanzo chake. 1Pe 2:21; 1Ak 11:1
Ayenera kulalikira kuti akwaniritse utumiki. 2Ti 4:2, 5; 1Ak 9:16
B. Zimene zimayeneretsa munthu kuti akhale mtumiki
Mzimu wa Mulungu ndiponso kudziwa Mawu ake. 2Ti 2:15; Yes 61:1-3
Kutsatira njira ya Khristu ya kulalikira. 1Pe 2:21; 2Ti 4:2, 5
Mulungu amaphunzitsa mwa mzimu ndi gulu lake. Yoh 14:26; 2Ak 3:1-3
30. Mzimu, Kukhulupirira Mizimu
A. Kodi mzimu woyera n’chiyani?
Ndi mphamvu yogwira ntchito ya Mulungu, si munthu ayi. Mac 2:2, 3, 33; Yoh 14:17
Anaugwiritsa ntchito polenga, pouzira Baibulo, ndi zina zotero. Ge 1:2; Eze 11:5
Umabala ndi kudzoza ziwalo za thupi la Khristu. Yoh 3:5-8; 2Ak 1:21, 22
Umapatsa mphamvu anthu a Mulungu ndi kuwatsogolera masiku ano. Aga 5:16, 18
B. Mphamvu imene imapangitsa zamoyo kukhala ndi moyo imatchedwa mzimu
Ndi mphamvu yopangitsa chamoyo kukhala moyo, imachirikizidwa ndi kupuma. Yak 2:26; Yob 27:3
Mulungu ndiye ali ndi ulamuliro pa mphamvu yochirikiza moyo imeneyi. Zek 12:1; Mla 8:8
Mphamvu yochirikiza moyo ya anthu, nyama, mwiniwake ndi Mulungu. Mla 3:19-21
Munthu akafa, ulamuliro pa mphamvu ya moyo umabwerera kwa Mulungu. Mla 12:7; Lu 23:46
C. Kukhulupirira mizimu kuyenera kupewedwa popeza ndi ntchito ya ziwanda
Mawu a Mulungu amaletsa. Yes 8:19, 20; Le 19:31; 20:6, 27
Kulosera ndiko kukhulupirira ziwanda, n’koletsedwa. Mac 16:16-18
Kumabweretsa chiwonongeko. Aga 5:19-21; Chv 21:8; 22:15
Kukhulupirira nyenyezi n’koletsedwa. De 18:10-12; Yer 10:2
31. Pemphero
A. Mapemphero amene Mulungu amamva
Mulungu amamvetsera mapemphero a anthu. Sl 145:18; 1Pe 3:12
Samvera mapemphero a osalungama kupatulapo akasintha njira yawo. Yes 1:15-17
Tiyenera kupemphera m’dzina la Yesu. Yoh 14:13, 14; 2Ak 1:20
Tiyenera kupemphera mogwirizana ndi chifuniro cha Mulungu. 1Yoh 5:14, 15
Chikhulupiriro n’chofunikira. Yak 1:6-8
B. Mapemphero obwerezabwereza, mapemphero opita kwa Mariya kapena kwa “oyera mtima” n’ngopanda pake
Tiyenera kupemphera kwa Mulungu m’dzina la Yesu. Yoh 14:6, 14; 16:23, 24
Mawu obwerezabwereza samvedwa. Mt 6:7
32. Sabata
A. Akhristu sakulamulidwa kusunga Sabata
Chilamulo chinathetsedwa pamaziko a imfa ya Yesu. Aef 2:15
Akhristu sakulamulidwa kusunga Sabata. Akl 2:16, 17; Aro 14:5, 10
Anadzudzulidwa chifukwa chosunga Sabata ndi zina zotero. Aga 4:9-11; Aro 10:2-4
Tiyenera kulowa mu mpumulo wa Mulungu mwa chikhulupiriro ndi kumvera. Ahe 4:9-11
B. Aisiraeli akale ndiwo okha anauzidwa kusunga Sabata
Sabata loyamba analisunga atayamba ulendo wawo waukulu. Eks 16:26, 27, 29, 30
Chinali chizindikiro chapadera kwa Aisiraeli. Eks 31:16, 17; Sl 147:19, 20
Chilamulo chinafunanso kuti azisunga zaka za Sabata. Eks 23:10, 11; Le 25:3, 4
Akhristu safunikira kusunga Sabata. Aro 14:5, 10; Aga 4:9-11
C. Sabata lopuma la Mulungu (tsiku la 7 la “mlungu” wolenga zinthu)
Linayamba atamaliza kulenga zinthu padziko lapansi. Ge 2:2, 3; Ahe 4:3-5
Linapitirira ngakhale pambuyo pa nthawi imene Yesu anali padziko lapansi. Ahe 4:6-8; Sl 95:7-9, 11
Akhristu amapuma pa ntchito zofuna kudzipindulitsa okha. Ahe 4:9, 10
Lidzatha Ufumu ukadzamaliza ntchito yake padziko lapansi. 1Ak 15:24, 28
33. Tchalitchi
A. Tchalitchi n’chauzimu, chomangidwa pa Khristu
Mulungu sakhala mu akachisi omangidwa ndi anthu. Mac 17:24, 25; 7:48
Tchalitchi choona ndicho kachisi wauzimu wa miyala yamoyo. 1Pe 2:5, 6
Khristu, mwala wa pakona. Atumwi, maziko achiwiri. Aef 2:20
Mulungu ayenera kulambiridwa ndi mzimu ndi choonadi. Yoh 4:24
B. Tchalitchi sichinamangidwe pa Petulo
Yesu sananene kuti tchalitchi chidzamangidwa pa Petulo. Mt 16:18
Yesu anatchulidwa kuti ndiye “thanthwe” limenelo. 1Ak 10:4
Petulo anati Yesu ndiye maziko. 1Pe 2:4, 6-8; Mac 4:8-12
34. Tchimo
A. Kodi tchimo n’chiyani?
Kuphwanya lamulo la Mulungu, kapena muyezo wake wangwiro. 1Yoh 3:4; 5:17
Munthu, pokhala cholengedwa cha Mulungu, ayenera kuyankha kwa iye. Aro 14:12; 2:12-15
Chilamulo chinadziwitsa uchimo, chinapangitsa anthu kuuzindikira. Aga 3:19; Aro 3:20
Tonse tili mu uchimo, ndife operewera pa muyezo wangwiro wa Mulungu. Aro 3:23; Sl 51:5
B. Chifukwa chimene tonse tikuvutikira ndi uchimo wa Adamu
Adamu anapatsira anthu onse kupanda ungwiro ndi imfa. Aro 5:12, 18
Mulungu anasonyeza chifundo polola anthu kukhalabe ndi moyo. Sl 103:8, 10, 14, 17
Nsembe ya Yesu imaphimba machimo. 1Yoh 2:2
Uchimo ndi ntchito zina zonse za Mdyerekezi zidzafafanizidwa. 1Yoh 3:8
C. Chipatso choletsedwa kunali kusamvera, sichinali kugonana
Lamulo loletsa kudya zipatso za mtengowo linaperekedwa Hava asanalengedwe. Ge 2:17, 18
Adamu ndi Hava anauzidwa kuti akhale ndi ana. Ge 1:28
Ana si chipatso cha uchimo, koma ndi dalitso la Mulungu. Sl 127:3-5
Hava anachimwa mwamuna wake ali kwina, iye ndiye anayamba kudya. Ge 3:6; 1Ti 2:11-14
Adamu, monga mutu, anapandukira lamulo la Mulungu. Aro 5:12, 19
D. Kodi kuchimwira mzimu n’chiyani? (Mt 12:32; Mko 3:28, 29)
Si tchimo lobadwa nalo ayi. Aro 5:8, 12, 18; 1Yoh 5:17
Munthu angamvetse chisoni mzimu woyera, n’kudzasintha. Aef 4:30; Yak 5:19, 20
Kuchita tchimo dala mobwerezabwereza kumabweretsa imfa. 1Yoh 3:6-9
Mulungu ndiye amaweruza oterowo, amawachotsera mzimu wake. Ahe 6:4-8
Sitiyenera kupempherera anthu osalapa oterowo. 1Yoh 5:16, 17
35. Ubatizo
A. Ndi wofunika kuti munthu akhale Mkhristu
Yesu anapereka chitsanzo. Mt 3:13-15; Ahe 10:7
N’chizindikiro cha kudzikana kapena kudzipereka kwa Mulungu. Mt 16:24; 1Pe 3:21
Ndi wa okhawo a msinkhu woti n’kuphunzitsidwa. Mt 28:19, 20; Mac 2:41
Kumizidwa m’madzi ndiko njira yoyenera. Mac 8:38, 39; Yoh 3:23
B. Suchotsa machimo
Yesu sanabatizidwe kuti achotse machimo. 1Pe 2:22; 3:18
Magazi a Yesu ndiwo amachotsa machimo. 1Yoh 1:7
36. Ufumu
A. Zimene Ufumu wa Mulungu udzachitire anthu
Udzakwaniritsa chifuniro cha Mulungu. Mt 6:9, 10; Sl 45:6; Chv 4:11
Ndi boma lokhala ndi mfumu ndi malamulo. Yes 9:6, 7; 2:3; Sl 72:1, 8
Udzachotsa zoipa zonse, udzalamulira dziko lonse lapansi. Da 2:44; Sl 72:8
Ulamuliro wa zaka 1,000 udzakonzanso anthu. Udzakonzanso Paradaiso. Chv 21:2-4; 20:6
B. Uyamba kugwira ntchito adani a Khristu akadalipo
Khristu ataukitsidwa anayembekeza kwa nthawi yaitali. Sl 110:1; Ahe 10:12, 13
Analandira mphamvu, anamenya nkhondo yolimbana ndi Satana. Sl 110:2; Chv 12:7-9; Lu 10:18
Ufumu unakhazikitsidwa pa nthawiyo, kenako padziko lapansi panagwa masoka. Chv 12:10, 12
Mavuto alipowa akutanthauza kuti ndi nthawi yoti tiime kumbali ya Ufumu. Chv 11:15-18
C. Suli ‘m’mitima,’ sunapangidwe ndi khama la anthu
Ufumuwo uli kumwamba, osati padziko lapansi. 2Ti 4:18; 1Ak 15:50; Sl 11:4
Suli ‘m’mitima,’ Yesu anali kulankhula kwa Afarisi. Lu 17:20, 21
Si mbali ya dziko lapansi. Yoh 18:36; Lu 4:5-8; Da 2:44
Maboma, mfundo zimene dzikoli limatsatira, zidzalowedwa m’malo. Da 2:44
37. Ukwati
A. Mgwirizano wa ukwati uyenera kukhala wolemekezeka
Umayerekezedwa ndi Khristu ndi mkwatibwi wake. Aef 5:22, 23
Pogona anthu okwatirana pasaipitsidwe. Ahe 13:4
Okwatirana akulangizidwa kusapatukana. 1Ak 7:10-16
Dama ndilo maziko okhawo a m’Malemba othetsera ukwati. Mt 19:9
B. Mfundo ya umutu iyenera kulemekezedwa ndi Akhristu
Monga mutu, mwamuna ayenera kukonda ndi kusamalira banja. Aef 5:23-31
Mkazi azigonjera, kukonda, ndi kumvera mwamuna wake. 1Pe 3:1-7; Aef 5:22
Ana akhale omvera. Aef 6:1-3; Akl 3:20
C. Udindo wa makolo achikhristu kwa ana awo
Kuwasonyeza chikondi, kukhala ndi nthawi yochita nawo zinthu, ndi kuwasamala. Tit 2:4
Musawakwiyitse. Akl 3:21
Muziwapezera zofunika, kuphatikizapo zinthu zauzimu. 2Ak 12:14; 1Ti 5:8
Aphunzitseni kuti adzathe kukhala ndi moyo wabwino. Aef 6:4; Miy 22:6, 15; 23:13, 14
D. Akhristu ayenera kukwatira Akhristu anzawo okha
Kwatirani “mwa Ambuye” basi. 1Ak 7:39; De 7:3, 4; Ne 13:26
E. Mitala siloledwa ndi Malemba
Dongosolo loyambirira linali lakuti mwamuna azikhala ndi mkazi mmodzi yekha. Ge 2:18, 22-25
Yesu anabwezeretsa muyezo umenewu kwa Akhristu. Mt 19:3-9
Akhristu oyambirira sanali kukwatira mitala. 1Ak 7:2, 12-16; Aef 5:28-31
38. Utatu
A. Mulungu, Atate, ndi mmodzi, wamkulu koposa m’chilengedwe chonse
Mulungu sali atatu mwa mmodzi. De 6:4; Mki 2:10; Mko 10:18; Aro 3:29, 30
Mwana anachita kulengedwa, Mulungu analiko yekha pa chiyambi. Chv 3:14; Akl 1:15; Yes 44:6
Mulungu ndiye wolamulira chilengedwe chonse nthawi zonse. Afi 2:5, 6; Da 4:35
Mulungu ayenera kulemekezedwa kuposa wina aliyense. Afi 2:10, 11
B. Mwana anali wamng’ono kwa Atate asanabwere padziko lapansi ndi pambuyo pake
Mwanayo anali womvera pamene anali kumwamba, anatumidwa ndi Atate. Yoh 8:42; 12:49
Padziko lapansi anali womvera, Atate anali wamkulu. Yoh 14:28; 5:19; Ahe 5:8
Kumwamba anamukweza n’kumupatsa udindo wapamwamba, koma anakhalabe pansi pa Atate wake. Afi 2:9; 1Ak 15:28; Mt 20:23
Yehova ndiye mutu wa Khristu, ndiye Mulungu wake. 1Ak 11:3; Yoh 20:17; Chv 1:6
C. Umodzi wa Mulungu ndi Khristu
Nthawi zonse amakhala ogwirizana kwathunthu. Yoh 8:28, 29; 14:10
Umodzi, monga wa mwamuna ndi mkazi wake. Yoh 10:30; Mt 19:4-6
Okhulupirira onse afunika kukhala ndi umodzi ngati umenewo. Yoh 17:20-22; 1Ak 1:10
Kulambira Yehova yekha kudzera mwa Khristu kudzakhalako kosatha. Yoh 4:23, 24
D. Mzimu woyera wa Mulungu ndi mphamvu yake yogwira ntchito
Ndi mphamvu, osati munthu. Mt 3:16; Yoh 20:22; Mac 2:4, 17, 33
Si munthu wokhala kumwamba pamodzi ndi Mulungu ndi Khristu. Mac 7:55, 56; Chv 7:10
Umayendetsedwa ndi Mulungu kuti ukwaniritse zolinga zake. Sl 104:30; 1Ak 12:4-11
Otumikira Mulungu amaulandira, umawatsogolera. 1Ak 2:12, 13; Aga 5:16
39. Yehova, Mulungu
A. Dzina la Mulungu
“Mulungu” ndi dzina laulemu chabe. Ambuye wathu ali ndi dzina lake lenileni. 1Ak 8:5, 6
Timapemphera kuti dzina lake liyeretsedwe. Mt 6:9, 10
Yehova ndilo dzina la Mulungu. Sl 83:18; Eks 6:2, 3; 3:15; Yes 42:8
Lilimo m’Baibulo la King James Version pa Eks 6:3
(m’mawu a m’munsi m’Baibulo la Douay Version). Sl 83:18; Yes 12:2; 26:4
Yesu anadziwitsa dzinalo. Yoh 17:6, 26; 5:43; 12:12, 13, 28
B. Mulungu aliko
N’zosatheka kuona Mulungu n’kukhalabe ndi moyo. Eks 33:20; Yoh 1:18; 1Yoh 4:12
Kuona Mulungu kuti tikhulupirire n’kosafunikira. Ahe 11:1; Aro 8:24, 25; 10:17
Mulungu amadziwika ndi ntchito zake zooneka. Aro 1:20; Sl 19:1, 2
Kukwaniritsidwa kwa maulosi ndi umboni wakuti Mulungu alikodi. Yes 46:8-11
C. Makhalidwe a Mulungu
Mulungu ndi chikondi. 1Yoh 4:8, 16; Eks 34:6; 2Ak 13:11; Mik 7:18
Ndi wopambana mu nzeru. Yob 12:13; Aro 11:33; 1Ak 2:7
Ndi wolungama, amaweruza molungama. De 32:4; Sl 37:28
Ndi wamphamvuyonse. Yob 37:23; Chv 7:12; 4:11
D. Sikuti anthu onse amatumikira Mulungu mmodzi
Njira yooneka yabwino, sikuti imakhala yolondola nthawi zonse. Miy 16:25; Mt 7:21
Pali misewu iwiri, umodzi wokha ndi umene ukupita ku moyo. Mt 7:13, 14; De 30:19
Pali milungu yambiri, koma Mulungu woona ndi mmodzi yekha. 1Ak 8:5, 6; Sl 82:1
Kudziwa Mulungu woona n’kofunika kuti tipeze moyo. Yoh 17:3; 1Yoh 5:20
40. Yesu
A. Yesu ndi Mwana wa Mulungu ndiponso Mfumu yoikidwa
Iye ndi woyamba kubadwa wa Mulungu,
anamugwiritsa ntchito polenga zinthu zina zonse. Chv 3:14; Akl 1:15-17
Anatumizidwa kudzabadwa monga munthu kwa mkazi, anakhala wotsikirapo kwa angelo. Aga 4:4; Ahe 2:9
Anabadwa mwa mzimu wa Mulungu, anali ndi tsogolo lokakhala kumwamba. Mt 3:16, 17
Anamukweza n’kumupatsa udindo wapamwamba kuposa umene anali nawo asanadzakhale munthu. Afi 2:9, 10
B. Kukhulupirira mwa Yesu Khristu n’kofunika kuti tidzapulumuke
Khristu ndiye Mbewu yolonjezedwa ya Abulahamu. Ge 22:18; Aga 3:16
Yesu yekha ndiye Mkulu wa Ansembe, dipo. 1Yoh 2:1, 2; Ahe 7:25, 26; Mt 20:28
Moyo umapezeka mwa kudziwa Mulungu ndi Khristu, kumvera. Yoh 17:3; Mac 4:12
C. Si kukhulupirira mwa Yesu kokha kumene kumafunika
Kukhulupirira kuzikhala ndi ntchito zake. Yak 2:17-26; 1:22-25
Tiyenera kumvera malamulo, kugwira ntchito imene anagwira. Yoh 14:12, 15; 1Yoh 2:3
Sikuti onse otchula dzina la Ambuye adzalowa mu Ufumu. Mt 7:21-23
41. Zifaniziro
A. Kugwiritsa ntchito zifaniziro polambira n’kutonza Mulungu
N’zosatheka kupanga chifaniziro cha Mulungu. 1Yoh 4:12; Yes 40:18; 46:5; Mac 17:29
Akhristu amachenjezedwa za zifaniziro. 1Ak 10:14; 1Yoh 5:21
Mulungu ayenera kulambiridwa ndi mzimu ndi choonadi. Yoh 4:24
B. Kulambira zifaniziro kunabweretsa imfa kwa mtundu wa Isiraeli
Ayuda analetsedwa kulambira zifaniziro. Eks 20:4, 5
Sizimva, sizilankhula. Ozipanga adzafanana nazo. Sl 115:4-8
Zinakhala msampha, zinabweretsa chiwonongeko. Sl 106:36, 40-42; Yer 22:8, 9
C. Kulambira Mulungu kudzera m’zifaniziro n’kosaloledwa
Mulungu anakana kuti anthu azimulambira pogwiritsa ntchito zifaniziro. Yes 42:8
Mulungu yekha ndiye “Wakumva pemphero.” Sl 65:1, 2
42. Zoipa, Mavuto a m’Dziko
A. Amene amachititsa mavuto m’dziko
Ulamuliro woipa ndi umene ukuchititsa kuti zinthu zikhale zoipa masiku ano. Miy 29:2; 28:28
Wolamulira dziko lapansili ndi mdani wa Mulungu. 2Ak 4:4; 1Yoh 5:19; Yoh 12:31
Mdyerekezi amachititsa masoka, nthawi yamuthera. Chv 12:9, 12
Mdyerekezi akadzamangidwa, padzakhala mtendere wochuluka. Chv 20:1-3; 21:3, 4
B. Chifukwa chake Mulungu walola kuti zoipa zizichitika
Mdyerekezi anatsutsa zakuti anthu angakhulupirike kwa Mulungu. Yob 1:11, 12
Okhulupirika amapatsidwa mwayi wosonyeza kukhulupirika kwawo. Aro 9:17; Miy 27:11
Mdyerekezi wapezeka kuti ndi wabodza, nkhaniyo idzathetsedwa. Yoh 12:31
Okhulupirika adzalandira mphoto ya moyo wosatha. Aro 2:6, 7; Chv 21:3-5
C. Kutalika kwa nthawi ya mapeto ndi chifundo cha Mulungu
Monga m’masiku a Nowa, kuchenjeza kumatenga nthawi. Mt 24:14, 37-39
Mulungu sakuchedwa, koma akusonyeza chifundo. 2Pe 3:9; Yes 30:18
Baibulo limatithandiza kuti tisadzadzidzimutsidwe. Lu 21:36; 1At 5:4
Panopa yesetsani kupeza njira imene Mulungu wapereka yokutetezerani. Yes 2:2-4; Zef 2:3
D. Njira yothetsera mavuto a dziko sidzachokera kwa anthu
Anthu ali ndi mantha aakulu, athedwa nzeru. Lu 21:10, 11; 2Ti 3:1-5
Ufumu wa Mulungu ndi umene udzapambane, osati anthu. Da 2:44; Mt 6:10
Kuti mukhale ndi moyo, yesetsani kukhala pa mtendere ndi Mfumu panopa. Sl 2:9, 11, 12
43. Zolembedweratu
A. Mulungu sanalemberetu tsogolo la munthu
Cholinga cha Mulungu n’chotsimikizirika. Yes 55:11; Ge 1:28
Munthu aliyense payekha ali ndi mwayi wosankha kutumikira Mulungu. Yoh 3:16; Afi 2:12