Genesis
6 Pamene anthu anayamba kuchuluka padziko lapansi, kunabadwa ana aakazi.+ 2 Ndiyeno ana a Mulungu+ woona anayamba kuona+ kuti ana aakazi a anthu anali okongola. Chotero, anayamba kudzitengera okha akazi alionse amene anawasankha. 3 Pambuyo pake, Yehova anati: “Mzimu wanga+ supitiriza mpaka kalekale kulezera mtima anthu,+ popeza alinso athupi.+ Choncho, masiku a moyo wawo adzangokhala zaka 120.”+
4 M’masiku amenewo ndiponso kupita m’tsogolo, padziko lapansi panali Anefili.* Pa nthawiyo, ana a Mulungu woona anali kugona ndi ana aakazi a anthu ndipo anawaberekera ana. Anawo anali ziphona zakalelo, amuna otchuka.
5 Pamenepo, Yehova anaona kuti kuipa kwa anthu kwachuluka padziko lapansi, ndipo malingaliro+ onse a m’mitima ya anthu anali oipa okhaokha nthawi zonse.+ 6 Chotero, Yehova anamva chisoni+ kuti anapanga anthu padziko lapansi, ndipo zinam’pweteka kwambiri mumtima.+ 7 Choncho Yehova anati: “Ndidzaseseratu padziko lapansi anthu amene ndinawalenga.+ Kuyambira munthu, nyama yoweta, nyama yokwawa, mpaka cholengedwa chouluka m’mlengalenga,+ chifukwa ndikumva chisoni kuti ndinazipanga.”+ 8 Koma Nowa anayanjidwa ndi Yehova.
9 Tsopano nayi mbiri ya Nowa.
Nowa anali munthu wolungama.+ Iye anali wopanda cholakwa pakati pa anthu a m’nthawi yake. Nowa anayenda ndi Mulungu woona.+ 10 M’kupita kwa nthawi, Nowa anabereka ana aamuna atatu, Semu, Hamu ndi Yafeti.+ 11 Koma dziko lapansi linali litaipa pamaso pa Mulungu woona,+ ndipo linadzaza ndi chiwawa.+ 12 Chotero, Mulungu poyang’ana dziko lapansi anaona kuti laipa,+ chifukwa njira za anthu onse zinali zitaipa.+
13 Pambuyo pake, Mulungu anauza Nowa kuti: “Nthawi yafika yakuti ndiwononge anthu onse,+ popeza dziko lapansi ladzaza ndi chiwawa chifukwa cha iwo. Choncho ndiwawonongera limodzi ndi dziko lapansi.+ 14 Udzipangire chingalawa cha mtengo wa mnjale.+ Uchigawe zipindazipinda, ndipo uchimate ndi phula+ mkati ndi kunja komwe. 15 Uchipange motere: M’litali chikhale mikono*+ 300, m’lifupi mikono 50, ndipo kutalika kwake kuyambira pansi mpaka pamwamba chikhale mikono 30. 16 Chingalawacho uchiike windo.* Windolo likhale la mpata wa mkono umodzi kuchokera kudenga* lake. Khomo la chingalawacho uliike m’mbali mwake.+ Chikhale cha nyumba zosanjikiza zitatu, yapansi, yapakati, ndi yapamwamba.
17 “Koma ine ndidzabweretsa chigumula+ chamadzi padziko lapansi, kuti chiwononge chamoyo+ chilichonse cha pansi pa thambo, chimene chili ndi mphamvu ya moyo* m’thupi mwake. Chilichonse cha m’dziko lapansi chidzafa.+ 18 Ndipo ndikupanga pangano ndi iwe. Iweyo udzalowe m’chingalawacho limodzi ndi ana ako, mkazi wako, ndi akazi a ana ako.+ 19 Udzalowetsenso m’chingalawacho chamoyo chilichonse cha mtundu uliwonse.+ Udzazilowetse ziwiriziwiri, champhongo ndi chachikazi, kuti zidzasungike zamoyo limodzi nawe.+ 20 Udzalowe nazo ziwiriziwiri za mtundu uliwonse. Zolengedwa zouluka monga mwa mitundu yawo, nyama zoweta monga mwa mitundu yawo,+ nyama zonse zokwawa panthaka monga mwa mitundu yawo, kuti zidzasungike zamoyo.+ 21 Koma iweyo udzatenge chakudya cha mtundu uliwonse chodyedwa.+ Udzachisonkhanitse kuti chidzakhale chakudya chanu ndi cha zamoyo zinazo.”+
22 Ndipo Nowa anachita zonse motsatira zimene Mulungu anamulamula. Anachitadi momwemo.+