1 Akorinto
1 Ine Paulo, woitanidwa kukhala mtumwi+ wa Yesu Khristu mwa chifuniro cha Mulungu,+ pamodzi ndi Sositene+ m’bale wathu, 2 ndikulembera mpingo wa Mulungu umene uli ku Korinto,+ kwa inu amene mwayeretsedwa+ mwa Khristu Yesu, amene mwaitanidwa kuti mukhale oyera,+ pamodzi ndi onse amene kulikonse akuitana pa dzina+ la Ambuye wathu, Yesu Khristu, Ambuye wawo ndiponso wathu.+
3 Kukoma mtima kwakukulu+ ndi mtendere+ zochokera kwa Mulungu Atate wathu ndi Yesu Khristu Ambuye wathu+ zikhale ndi inu.
4 Nthawi zonse ndimayamika Mulungu chifukwa cha inu, poona kukoma mtima kwakukulu+ kwa Mulungu kumene anakusonyezani kudzera mwa Khristu Yesu,+ 5 kuti mwa iye mwakhala olemera+ m’zinthu zonse, pokhala ndi mphamvu zonse za kulankhula ndi kudziwa zinthu zonse,+ 6 popeza kuti umboni wonena za Khristu+ wakhazikika pakati pa inu, 7 moti palibe mphatso+ imene ikuperewera mwa inu, pamene mukudikira mwachidwi kuululidwa+ kwa Ambuye wathu Yesu Khristu. 8 Mulungu adzakulimbitsani+ mpaka pa mapeto, kuti musakhale ndi chifukwa chokunenezerani+ m’tsiku+ la Ambuye wathu Yesu Khristu.+ 9 Mulungu amene anakuitanani kuti mukhale oyanjana+ ndi Mwana wake Yesu Khristu, Ambuye wathu, ndi wokhulupirika.+
10 Tsopano ndikukudandaulirani+ abale, m’dzina+ la Ambuye wathu Yesu Khristu, kuti nonse muzilankhula mogwirizana ndi kuti pasakhale magawano+ pakati panu, koma kuti mukhale ogwirizana+ pokhala ndi mtima umodzi ndi maganizo amodzi.+ 11 Pakuti a m’banja la Kuloe andiuza+ za inu, abale anga, kuti pali magawano pakati panu. 12 Ndikutanthauza kuti, ena mwa inu amanena kuti: “Ine ndine wa Paulo,” ena amati, “Ine ndine wa Apolo,”+ enanso amati “Ine ndine wa Kefa,” pamene ena amati, “Ine ndine wa Khristu.” 13 Choncho Khristu wakhala wogawanika.+ Paulo sanapachikidwe chifukwa cha inu, anatero kodi? Kapena kodi munabatizidwa+ m’dzina la Paulo? 14 Ndikusangalala kuti sindinabatize aliyense wa inu kupatulapo Kirisipo+ ndi Gayo,+ 15 moti wina sanganene kuti munabatizidwa m’dzina langa. 16 Inde, ndinabatizanso banja la Sitefana.+ Koma za enawo, sindikudziwa ngati ndinabatizapo aliyense. 17 Pakuti Khristu sananditume+ kukabatiza anthu, koma kukalengeza uthenga wabwino, osati mwa nzeru za kulankhula,+ kuti mtengo wozunzikirapo* wa Khristu ungakhale wopanda pake.
18 Nkhani yokhudza mtengo wozunzikirapowo ndi chinthu chopusa+ kwa anthu amene akupita kukawonongedwa,+ koma kwa ife amene tikupulumutsidwa+ ndi mphamvu ya Mulungu.+ 19 Pakuti Malemba amati: “Ndidzathetsa nzeru zonse za anthu anzeru,+ ndipo ndidzakankhira pambali+ kuchenjera kwa anthu ophunzira.”+ 20 Kodi wanzeru ali kuti? Mlembi ali kuti?+ Katswiri wa mtsutso+ wa nthawi* ino ali kuti?+ Kodi Mulungu sanapange nzeru za dzikoli kukhala zopusa?+ 21 Pakuti ngakhale kuti dziko mwa nzeru zake+ silinathe kumudziwa Mulungu,+ kunamukomera Mulungu mwa nzeru zake kupulumutsa okhulupirira kudzera mu nkhani yopusayo,+ imene ikulalikidwa.
22 Pakuti Ayuda amafuna kuona zizindikiro+ ndipo Agiriki amafunafuna nzeru,+ 23 koma ife timalalikira za Khristu amene anapachikidwa.+ Kwa Ayuda, chimenechi ndi chinthu chokhumudwitsa+ ndipo kwa mitundu ina ndi kupusa.+ 24 Ngakhale zili choncho, kwa amene anaitanidwa, Ayuda ndiponso Agiriki, Khristu ndiye mphamvu+ ya Mulungu ndi nzeru+ za Mulungu. 25 Pakuti chinthu chopusa cha Mulungu ndi chanzeru kuposa anthu, ndipo chinthu chofooka cha Mulungu n’champhamvu kuposa anthu.+
26 Mukuona mmene anakuitanirani, abale, kuti si ambiri amene anthu amawaona kuti ndi anzeru+ omwe anaitanidwa,+ si ambiri amphamvu+ amene anaitanidwa, si ambiri a m’mabanja achifumu. 27 Koma Mulungu anasankha zopusa za dziko+ kuti achititse manyazi anthu anzeru, ndipo Mulungu anasankha zinthu zofooka za dziko kuti achititse manyazi+ zinthu zamphamvu. 28 Mulungu anasankha zinthu zonyozeka za dziko ndi zinthu zimene anthu amaziona ngati zachabechabe, zinthu zimene palibe,+ kuti athetse+ mphamvu zinthu zimene zilipo, 29 kuti pasapezeke munthu wodzitama+ pamaso pa Mulungu. 30 Koma inu muli ogwirizana ndi Khristu Yesu chifukwa cha Mulunguyo. Yesuyo amatisonyeza nzeru+ za Mulungu ndiponso chilungamo+ cha Mulungu. Kudzera mwa Yesu, anthu akhoza kuyeretsedwa,+ ndipo kudzera mwa dipo* akhoza kumasulidwa,+ 31 kuti zikhale monga Malemba amanenera kuti: “Amene akudzitama, adzitame mwa Yehova.”+