א [ʼAʹleph]
119 Odala ndi anthu osalakwitsa kanthu m’njira zawo,+
Anthu amene akutsatira chilamulo cha Yehova.+
2 Odala ndi anthu amene amasunga zikumbutso zake,+
Amene amayesetsa kumufunafuna ndi mtima wonse.+
3 Ndithu, iwo sachita chinthu chosalungama.+
Amayenda m’njira zake.+
4 Inu mwatilamula kuti tisunge+
Malamulo anu mosamala.+
5 Haa! Ndikanakonda kuti ndiyende mowongoka+
Kuti ndisunge malangizo anu,+
6 Pamenepo sindikanachita manyazi,+
Pamene ndikulabadira malamulo anu onse.+
7 Ndidzakutamandani ndi mtima wowongoka,+
Pamene ndikuphunzira zigamulo zanu zolungama.+
8 Ndikupitiriza kusunga malangizo anu,+
Choncho musandisiyiretu.+
ב [Behth]
9 Kodi wachinyamata+ angakhale bwanji woyera pa moyo wake?
Mwa kudziyang’anira ndi kuchita zinthu mogwirizana ndi mawu anu.+
10 Ndayesetsa kukufunafunani ndi mtima wanga wonse.+
Musandichititse kusochera ndi kuchoka pa malamulo anu.+
11 Ndasunga mosamala mawu anu mumtima mwanga,+
Kuti ndisakuchimwireni.+
12 Ndinu wodala inu Yehova.
Ndiphunzitseni malamulo anu.+
13 Ndi milomo yanga ndalengeza+
Zigamulo zonse zotuluka pakamwa panu.+
14 Ndimakondwera kuyenda m’njira ya zikumbutso zanu,+
Ngati mmene anthu amachitira akapeza chuma chilichonse chamtengo wapatali.+
15 Ndidzasinkhasinkha malamulo anu,+
Ndipo ndidzalabadira njira zanu.+
16 Ndidzakonda malamulo anu.+
Ndipo sindidzaiwala mawu anu.+
ג [Giʹmel]
17 Ndichitireni zabwino, ine mtumiki wanu, kuti ndikhale ndi moyo,+
Ndi kuti ndisunge mawu anu.+
18 Tsegulani maso anga kuti ndione+
Zinthu zodabwitsa za m’chilamulo chanu.+
19 Ine ndine mlendo m’dziko ili.+
Musandibisire malamulo anu.+
20 Moyo wanga wasautsika chifukwa cholakalaka+
Zigamulo zanu nthawi zonse.+
21 Mwadzudzula odzikuza otembereredwa,+
Amene akusochera ndi kuchoka pa malamulo anu.+
22 Mugubuduze ndi kuchotsa chitonzo ndi kunyozedwa kwanga,+
Pakuti ndasunga zikumbutso zanu.+
23 Akalonga asonkhana pamodzi kuti akambirane zondiukira.+
Koma ine mtumiki wanu, ndimasinkhasinkha malangizo anu.+
24 Ndimakonda zikumbutso zanu,+
Ndipo zili ngati anthu amene amandipatsa malangizo.+
ד [Daʹleth]
25 Moyo wanga wamamatira kufumbi.+
Ndisungeni wamoyo mogwirizana ndi mawu anu.+
26 Ndakuuzani za njira zanga kuti mundiyankhe.+
Ndiphunzitseni malamulo anu.+
27 Ndithandizeni kumvetsa njira zofotokozedwa m’malamulo anu,+
Kuti ndisinkhesinkhe ntchito zanu zodabwitsa.+
28 Ine ndikusowa tulo chifukwa cha chisoni.+
Ndilimbitseni ndi mawu anu.+
29 Ndichotsereni njira yolakwika,+
Ndikomereni mtima mwa kundipatsa chilamulo chanu.+
30 Ine ndasankha kuyenda mokhulupirika.+
Zigamulo zanu ndimaziona kukhala zoyenera.+
31 Ndamamatira zikumbutso zanu.+
Inu Yehova, musandichititse manyazi.+
32 Ndidzamvera malamulo anu,+
Chifukwa mwandichititsa kuwamvetsa bwino.+
ה [Heʼ]
33 Ndilangizeni inu Yehova, kuti ndiyende motsatira malangizo anu,+
Kuti nditsatire malangizo anu moyo wanga wonse.+
34 Ndithandizeni kukhala wozindikira kuti nditsatire chilamulo chanu,+
Ndiponso kuti ndichisunge ndi mtima wonse.+
35 Ndiyendetseni m’njira ya malamulo anu,+
Pakuti ndikukondwera ndi njira imeneyi.+
36 Ndithandizeni kuti mtima wanga uziganizira zikumbutso zanu,+
Osati kupeza phindu.+
37 Chititsani maso anga kuti asaone zinthu zopanda pake.+
Ndiyendetseni m’njira yanu kuti ndikhalebe wamoyo.+
38 Kwaniritsani mawu anu pa mtumiki wanu,+
Mawu amene amachititsa mtumiki wanu kukuopani.+
39 Ndichotsereni chitonzo chimene ndikuchiopa,+
Pakuti zigamulo zanu ndi zabwino.+
40 Taonani! Ine ndikulakalaka malamulo anu.+
Ndisungeni wamoyo mogwirizana ndi chilungamo chanu.+
ו [Waw]
41 Monga mwa mawu anu, inu Yehova, ndipatseni chipulumutso chanu.+
Ndipatseni zochita zanu zosonyeza kukoma mtima kosatha,+
42 Kuti ndipeze choyankha kwa wonditonza,+
Pakuti ine ndakhulupirira mawu anu.+
43 Musachotse mawu a choonadi pakamwa panga,+
Pakuti ndayembekezera chigamulo chanu.+
44 Ndidzasunga chilamulo chanu nthawi zonse,+
Mpaka kalekale, ndithu mpaka muyaya.+
45 Ndidzayenda uku ndi uku m’malo otakasuka,+
Chifukwa ndaphunzira malamulo anu ndi kuwasunga.+
46 Komanso ndidzanena za zikumbutso zanu pamaso pa mafumu,+
Ndipo sindidzachita manyazi.+
47 Ndidzakondwera ndi malamulo anu+
Amene ndimawakonda.+
48 Ndidzapemphera kwa inu nditakweza manja anga chifukwa ndimakonda malamulo anu,+
Ndipo ndidzasinkhasinkha malangizo anu.+
ז [Zaʹyin]
49 Kumbukirani mawu amene munandiuza ine mtumiki wanu,+
Mawu amene ndikuwayembekezera malinga ndi lonjezo lanu.+
50 Chimenechi ndi chilimbikitso changa mu nsautso yanga,+
Pakuti mawu anu andisungabe wamoyo.+
51 Anthu odzikuza andinyoza koopsa.+
Koma ine sindinapatuke pa chilamulo chanu.+
52 Ndimakumbukira zigamulo zanu zakalekale inu Yehova,+
Ndipo zimandilimbikitsa.+
53 Mkwiyo ukuyaka mumtima mwanga chifukwa cha oipa,+
Amene akusiya chilamulo chanu.+
54 Kwa ine, malangizo anu akhala ngati nyimbo zokutamandani,+
M’nyumba zimene ndimakhala m’mayiko achilendo.+
55 Usiku ndimakumbukira dzina lanu, inu Yehova,+
Kuti ndisunge chilamulo chanu.+
56 Ndi zimenetu zandichitikira ine,
Chifukwa ndimatsatira malamulo anu.+
ח [Chehth]
57 Yehova, inu ndiye cholowa changa.+
Ndalonjeza kusunga mawu anu.+
58 Ndayesetsa ndi mtima wanga wonse kuti mundiyanje.+
Ndikomereni mtima monga mwa mawu anu.+
59 Ndaganizira mozama za njira zanga,+
Kuti mapazi anga ndiwabwezere ku zikumbutso zanu.+
60 Ndinafulumira ndipo sindinazengereze+
Kusunga malamulo anu.+
61 Zingwe za oipa zinandikulunga,+
Koma ine sindinaiwale chilamulo chanu.+
62 Pakati pa usiku ndimadzuka kuti ndikuyamikeni+
Chifukwa cha zigamulo zanu zolungama.+
63 Ine ndine mnzawo wa anthu okuopani,+
Ndiponso wa anthu osunga malamulo anu.+
64 Inu Yehova, kukoma mtima kwanu kosatha kwadzaza dziko lonse lapansi.+
Ndiphunzitseni malamulo anu.+
ט [Tehth]
65 Inu Yehova, mwandichitiradi zabwino ine mtumiki wanu,+
Monga mwa mawu anu.+
66 Ndiphunzitseni kuchita zabwino,+ kulingalira bwino+ ndi kudziwa zinthu,+
Pakuti ndimakhulupirira malamulo anu.+
67 Ndisanagwe m’masautso ndinali kuchimwa mosadziwa,+
Koma tsopano ndimasunga mawu anu.+
68 Inu ndinu wabwino ndipo mukuchita zabwino.+
Ndiphunzitseni malamulo anu.+
69 Anthu odzikuza andinenera mabodza ambiri,+
Koma ine ndidzasunga malamulo anu ndi mtima wanga wonse.+
70 Mitima yawo yauma ngati mafuta oundana,+
Koma ine ndimakonda chilamulo chanu.+
71 Zili bwino kuti ndasautsika,+
Kuti ndiphunzire malamulo anu.+
72 Chilamulo+ chotuluka pakamwa panu n’chabwino kwa ine,+
N’chabwino kwambiri kuposa ndalama masauzande zagolide ndi zasiliva.+
י [Yohdh]
73 Manja anu anandipanga, ndipo anandiumba.+
Ndithandizeni kukhala wozindikira, kuti ndiphunzire malamulo anu.+
74 Oopa inu ndi amene amasangalala akandiona,+
Chifukwa ndayembekezera mawu anu.+
75 Inu Yehova, ndikudziwa bwino kuti zigamulo zanu ndi zolungama,+
Ndiponso kuti mwandilanga chifukwa chakuti ndinu wokhulupirika.+
76 Kukoma mtima kwanu kosatha kundilimbikitse,+
Monga mwa mawu anu kwa ine mtumiki wanu.+
77 Ndisonyezeni chifundo chanu kuti ndikhalebe ndi moyo,+
Pakuti ndimakonda chilamulo chanu.+
78 Odzikuza achite manyazi, chifukwa andisocheretsa popanda chifukwa,+
Koma ine ndimasinkhasinkha malamulo anu.+
79 Anthu okuopani abwerere kwa ine,+
Chimodzimodzinso odziwa zikumbutso zanu.+
80 Mtima wanga usunge malangizo anu mosalakwitsa kanthu,+
Kuti ndisachite manyazi.+
כ [Kaph]
81 Ine ndafooka chifukwa cholakalaka chipulumutso chanu,+
Pakuti ndayembekezera mawu anu.+
82 Maso anga alefuka chifukwa cholakalaka mawu anu,+
Ndipo ndikunena kuti: “Kodi mudzandilimbikitsa liti?”+
83 Ndakhala ngati thumba lachikopa+ mu utsi,
Koma sindinaiwale malangizo anu.+
84 Kodi ine mtumiki wanu ndidikira kufikira liti?+
Kodi anthu ondizunza mudzawaweruza liti?+
85 Anthu amene sachita zinthu mogwirizana ndi chilamulo chanu,+
Anthu odzikuza akumba mbuna kuti andigwire.+
86 Malamulo anu onse ndi odalirika.+
Odzikuza andizunza popanda chifukwa. Chonde, ndithandizeni.+
87 Iwo anangotsala pang’ono kundifafaniza padziko lapansi,+
Koma ine sindinasiye malamulo anu.+
88 Ndisungeni wamoyo monga mwa kukoma mtima kwanu kosatha,+
Kuti ndisunge zikumbutso zotuluka pakamwa panu.+
ל [Laʹmedh]
89 Inu Yehova, mawu anu anakhazikika kumwamba,+
Mpaka kalekale.+
90 Kukhulupirika kwanu kudzakhalapobe ku mibadwomibadwo.+
Mwakhazikitsa mwamphamvu dziko lapansi, kuti lisagwedezeke.+
91 Chilengedwe chonse chakhalapobe kufikira lero chifukwa cha zigamulo zanu,+
Pakuti chilengedwe chonse chimakutumikirani.+
92 Ndikanapanda kukonda chilamulo chanu,+
Ndikanatheratu m’masautso anga.+
93 Sindidzaiwala malamulo anu mpaka kalekale,+
Chifukwa mwandisungabe wamoyo kudzera m’malamulo amenewo.+
94 Ine ndine wanu. Chonde ndipulumutseni,+
Chifukwa ndaphunzira malamulo anu ndi kuwasunga.+
95 Oipa amandiyembekezera kuti andiwononge,+
Koma ine ndimamvetsera zikumbutso zanu.+
96 Ndaona kuti zinthu zonse zabwino kwambiri zili ndi malire.+
Koma malamulo anu amakhudza mbali zonse.
מ [Mem]
97 Ndimakonda kwambiri chilamulo chanu!+
Ndimasinkhasinkha chilamulocho tsiku lonse.+
98 Malamulo anu amandichititsa kukhala wanzeru kuposa adani anga,+
Chifukwa ndi anga mpaka kalekale.+
99 Ndakhala wozindikira kwambiri kuposa aphunzitsi anga,+
Chifukwa ndimasinkhasinkha zikumbutso zanu.+
100 Ndimachita zinthu mozindikira kuposa anthu achikulire,+
Chifukwa ndimasunga malamulo anu.+
101 Ndaletsa mapazi anga kuyenda m’njira iliyonse yoipa.+
Ndachita izi kuti ndisunge mawu anu.+
102 Sindinapatuke pa zigamulo zanu,+
Pakuti inu mwandilangiza.+
103 Mawu anu amatsekemera m’kamwa mwanga,
Kuposa mmene uchi umakomera!+
104 Chifukwa cha malamulo anu ndimachita zinthu mozindikira.+
N’chifukwa chake ndimadana ndi njira iliyonse yachinyengo.+
נ [Nun]
105 Mawu anu ndi nyale younikira kumapazi anga,+
Ndi kuwala kounikira njira yanga.+
106 Ndalumbira kuti ndidzasunga zigamulo zanu zolungama,+
Ndipo ndidzakwaniritsa lumbiro langa.+
107 Ndasautsika kwambiri.+
Inu Yehova, ndisungenibe wamoyo monga mwa mawu anu.+
108 Inu Yehova, chonde kondwerani ndi nsembe zaufulu za pakamwa panga,+
Ndipo ndiphunzitseni zigamulo zanu.+
109 Moyo wanga uli pangozi nthawi zonse,+
Koma sindinaiwale chilamulo chanu.+
110 Oipa anditchera msampha,+
Koma ine sindinasochere ndi kuchoka pa malamulo anu.+
111 Ndatenga zikumbutso zanu kukhala chuma changa mpaka kalekale,+
Pakuti zimakondweretsa mtima wanga.+
112 Ndatsimikiza mtima kutsatira malangizo anu,+
Mpaka kalekale, ndithu kwa moyo wanga wonse.+
ס [Saʹmekh]
113 Ndimadana ndi anthu amitima iwiri,+
Koma ndimakonda chilamulo chanu.+
114 Inu ndinu malo anga obisalamo ndi chishango changa,+
Pakuti ndayembekezera mawu anu.+
115 Ndichokereni anthu ochita zoipa inu,+
Kuti ndisunge malamulo a Mulungu wanga.+
116 Inu Mulungu, ndithandizeni monga mwa mawu anu kuti ndikhalebe ndi moyo,+
Ndipo musandichititse manyazi chifukwa cha chiyembekezo changa.+
117 Ndithandizeni kuti ndipulumutsidwe,+
Ndipo ndidzamvera malangizo anu nthawi zonse.+
118 Onse osochera ndi kuchoka pa malangizo anu mwawataya kutali,+
Pakuti ndi achinyengo komanso onama.+
119 Anthu onse oipa mwawachotsa padziko lapansi ngati zonyansa.+
N’chifukwa chake ine ndimakonda zikumbutso zanu.+
120 Chifukwa choopa inu, thupi langa linagwidwa nthumanzi,+
Ndipo chifukwa cha zigamulo zanu, ndinachita mantha.+
ע [ʽAʹyin]
121 Ndapereka ziweruzo zolungama ndipo ndachita zinthu mwachilungamo.+
Musandipereke kwa anthu ondichitira chinyengo.+
122 Khalani ngati chikole kwa ine mtumiki wanu kuti mudzandichitira zabwino.+
Anthu odzikuza asandichitire chinyengo.+
123 Maso anga afooka chifukwa cholakalaka chipulumutso chanu+
Ndi mawu anu olungama.+
124 Ndichitireni zabwino ine mtumiki wanu monga mwa kukoma mtima kwanu kosatha,+
Ndipo ndiphunzitseni malamulo anu.+
125 Ine ndine mtumiki wanu.+ Ndithandizeni kukhala wozindikira,+
Kuti ndidziwe zikumbutso zanu.+
126 Ino ndi nthawi yakuti inu Yehova muchitepo kanthu,+
Chifukwa anthu odzikuzawo aphwanya chilamulo chanu.+
127 N’chifukwa chake ine ndimakonda malamulo anu+
Kuposa golide, golide woyenga bwino.+
128 Choncho ndaona kuti malamulo anu onse okhudza chilichonse ndi olungama.+
Ndimadana ndi njira iliyonse yachinyengo.+
פ [Peʼ]
129 Zikumbutso zanu n’zodabwitsa.+
N’chifukwa chake ine ndimazisunga.+
130 Kuululidwa kwa mawu anu kumapereka kuwala,+
Kumathandiza anthu osadziwa zambiri kukhala ozindikira.+
131 Ndatsegula kwambiri pakamwa panga kuti ndipume mofulumira,+
Chifukwa ndikulakalaka malamulo anu.+
132 Ndicheukireni ndi kundikomera mtima,+
Mogwirizana ndi zigamulo zimene mumapereka kwa anthu okonda dzina lanu.+
133 Mwapondetsa mwamphamvu mapazi anga pa mawu anu,+
Ndipo musalole kuti choipa chilichonse chindilamulire.+
134 Ndiwomboleni kwa munthu aliyense wondichitira zachinyengo,+
Ndipo ine ndidzasunga malamulo anu.+
135 Ndikomereni mtima ine mtumiki wanu,+
Ndipo ndiphunzitseni malamulo anu.+
136 Misozi yatsika m’maso mwanga ngati mitsinje ya madzi,+
Chifukwa chakuti iwo sanasunge chilamulo chanu.+
צ [Tsa·dhehʹ]
137 Ndinu wolungama inu Yehova,+
Ndipo zigamulo zanu ndi zowongoka.+
138 M’chilungamo chanu ndiponso kukhulupirika kwanu kosaneneka+
Mwatilamula kuti tisunge zikumbutso zanu.+
139 Changu changa chandidya,+
Chifukwa adani anga aiwala mawu anu.+
140 Mawu anu ndi oyengeka kwambiri,+
Ndipo ine mtumiki wanu ndimawakonda.+
141 Kwa ena ndine wopanda pake ndi wonyozeka.+
Koma sindinaiwale malamulo anu.+
142 Chilungamo chanu ndi chilungamo mpaka kalekale,+
Ndipo chilamulo chanu ndi choonadi.+
143 Zowawa ndi zovuta zinandigwera.+
Koma ndinakonda malamulo anu.+
144 Zikumbutso zanu zidzakhalabe zolungama mpaka kalekale.+
Ndithandizeni kukhala wozindikira kuti ndikhalebe ndi moyo.+
ק [Qohph]
145 Ndaitana ndi mtima wanga wonse.+ Ndiyankheni inu Yehova.+
Ndidzasunga malangizo anu.+
146 Ndakuitanani. Ndipulumutseni chonde!+
Ndidzasunga zikumbutso zanu.+
147 Ndadzuka m’mawa kuli mbuu,+ kuti ndipemphe thandizo kwa inu,+
Pakuti ndayembekezera mawu anu.+
148 Ndimadzuka pa ulonda wa usiku,+
Kuti ndisinkhesinkhe mawu anu.+
149 Imvani mawu anga mwa kukoma mtima kwanu kosatha.+
Inu Yehova, ndisungenibe wamoyo mogwirizana ndi zigamulo zanu.+
150 Okonda kuchita khalidwe lotayirira+ abwera pafupi ndi ine.
Iwo atalikirana kwambiri ndi chilamulo chanu.+
151 Inu Yehova muli pafupi,+
Ndipo malamulo anu onse ndi choonadi.+
152 Zina mwa zikumbutso zanu ndinazidziwa kale kwambiri,+
Pakuti munazikhazikitsa kalekale.+
ר [Rehsh]
153 Onani kusautsika kwanga ndipo ndipulumutseni,+
Pakuti sindinaiwale chilamulo chanu.+
154 Ndiyankhireni mlandu wanga ndi kundipulumutsa.+
Ndisungeni wamoyo mogwirizana ndi mawu anu.+
155 Chipulumutso chili kutali ndi anthu oipa,+
Pakuti sanaphunzire malamulo anu ndi kuwasunga.+
156 Chifundo chanu n’chachikulu, inu Yehova.+
Ndisungenibe wamoyo mogwirizana ndi zigamulo zanu.+
157 Anthu ondizunza komanso adani anga ndi ambiri.+
Koma ine sindinapatuke pa zikumbutso zanu.+
158 Ndaona anthu ochita zinthu mwachinyengo,+
Ndipo amandinyansa chifukwa sasunga mawu anu.+
159 Onani kuti ndimakonda malamulo anu.+
Inu Yehova, ndisungenibe wamoyo mwa kukoma mtima kwanu kosatha.+
160 Mawu anu onse ndi choonadi chokhachokha,+
Ndipo chigamulo chanu chilichonse cholungama chidzakhalapo mpaka kalekale.+
ש [Sin] kapena kuti [Shin]
161 Akalonga andizunza popanda chifukwa,+
Koma mtima wanga umaopa mawu anu.+
162 Ndikukondwera chifukwa cha mawu anu,+
Monga mmene munthu amachitira akapeza zofunkha zambiri.+
163 Ndimadana ndi chinyengo+ ndipo chimandinyansa,+
Koma ndimakonda chilamulo chanu.+
164 Ndimakutamandani maulendo 7 pa tsiku,+
Chifukwa cha zigamulo zanu zolungama.+
165 Okonda chilamulo chanu amapeza mtendere wochuluka,+
Ndipo palibe chowakhumudwitsa.+
166 Ndayembekezera chipulumutso chanu, inu Yehova,+
Ndipo ndatsatira malamulo anu.+
167 Ndasunga zikumbutso zanu,+
Ndipo ndimazikonda kwambiri.+
168 Ndasunga malamulo anu ndi zikumbutso zanu,+
Pakuti njira zanga zonse zili pamaso panu.+
ת [Taw]
169 Inu Yehova, imvani kulira kwanga kochonderera.+
Ndithandizeni kuti ndikhale wozindikira, monga mwa mawu anu.+
170 Pempho langa lakuti mundichitire chifundo lifike kwa inu.+
Ndipulumutseni monga mwa mawu anu.+
171 Milomo yanga itulutse mawu okutamandani,+
Pakuti mwandiphunzitsa malamulo anu.+
172 Lilime langa liimbe za mawu anu,+
Pakuti malamulo anu onse ndi olungama.+
173 Dzanja lanu lindithandize,+
Chifukwa ndasankha malamulo anu.+
174 Ndikulakalaka chipulumutso chanu, inu Yehova,+
Ndipo ndimakonda kwambiri chilamulo chanu.+
175 Ndisungenibe wamoyo kuti ndikutamandeni,+
Zigamulo zanu zindithandize.+
176 Ndayendayenda ngati nkhosa yosochera.+ Ndifunefuneni ine mtumiki wanu,+
Pakuti sindinaiwale malamulo anu.+