Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • Levitiko 18:17
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 17 “‘Ukakwatira mkazi, usavule mwana wake wamkazi.+ Usatenge mwana wamkazi wa mwana wamwamuna wa mkazi wakoyo kuti um’vule. Usatengenso mwana wamkazi wa mwana wake wamkazi kuti um’vule. Limeneli ndi khalidwe lotayirira+ chifukwa amenewa ndi achibale.

  • Oweruza 20:6
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 6 Choncho ndinatenga mdzakazi wanga ndi kum’duladula, n’kutumiza ziwalozo m’dera lililonse la cholowa cha Isiraeli.+ Ndinatero chifukwa iwo anachita khalidwe lotayirira+ komanso chinthu chopusa ndi chochititsa manyazi mu Isiraeli.+

  • Salimo 26:10
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 10 M’manja mwa anthu amenewa muli khalidwe lotayirira,+

      Ndipo m’dzanja lawo lamanja mwadzaza ziphuphu.+

  • Miyambo 10:23
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 23 Kwa wopusa, kusonyeza khalidwe lotayirira kuli ngati masewera,+ koma nzeru zimakhala ndi munthu wozindikira.+

  • Miyambo 21:27
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 27 Nsembe ya anthu oipa ndi yonyansa.+ Ndiye kuli bwanji munthu akaiperekera limodzi ndi makhalidwe otayirira?+

  • Agalatiya 5:19
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 19 Tsopano, ntchito za thupi zimaonekera.+ Ntchitozi ndizo dama,*+ zinthu zodetsa, khalidwe lotayirira,+

  • 2 Petulo 2:2
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 2 Kuwonjezera apo, ambiri adzatsatira+ khalidwe lotayirira+ la aphunzitsiwo, ndipo chifukwa cha amenewa, anthu adzalankhula monyoza njira ya choonadi.+

  • Yuda 4
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 4 Ndatero chifukwa chakuti anthu ena alowa mozemba pakati pathu.+ Anthu amenewa Malemba anawasonyezeratu kalekale+ kuti adzaweruzidwa.+ Iwo ndiwo anthu osaopa Mulungu+ amene atenga kukoma mtima kwakukulu kwa Mulungu wathu kukhala chifukwa chochitira khalidwe lotayirira,+ ndipo akhala osakhulupirika+ kwa Ambuye wathu mmodzi yekha+ amene anatigula,+ Yesu Khristu.

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena