Agalatiya
5 Khristu anatimasula kuti tikhale ndi ufulu umenewu.+ Chotero khalani olimba,+ ndipo musalole kumangidwanso m’goli laukapolo.+
2 Tamverani! Ine Paulo, ndikukuuzani kuti mukadulidwa,+ Khristu sadzakhala waphindu kwa inu. 3 Kuwonjezera apo, ndikunenetsa kwa munthu aliyense amene akudulidwa, kuti afunikanso kuchita zonse za m’Chilamulo.+ 4 Inuyo amene mukufuna kuyesedwa olungama mwa chilamulo, mwadzilekanitsa ndi Khristu,+ kaya mukhale ndani, mwagwera kunja kwa kukoma mtima kwake kwakukulu.+ 5 Koma kudzera mwa mzimu, ife tikuyembekezera mwachidwi chilungamo cholonjezedwacho, chimene chimadza mwa chikhulupiriro.+ 6 Pakuti kwa Khristu Yesu, kudulidwa kapena kusadulidwa zilibe phindu,+ koma chikhulupiriro+ chimene chimagwira ntchito kudzera m’chikondi.+
7 Munali kuthamanga bwino.+ Anakusokonezani ndani kuti musapitirize kumvera choonadi?+ 8 Kukopeka kumeneku sikunachokere kwa Iye amene anakuitanani.+ 9 Chofufumitsa chaching’ono chimafufumitsa mtanda wonse.+ 10 Ndikukhulupirira+ kuti inu amene muli ogwirizana+ ndi Ambuye, simudzasintha maganizo, koma munthu amene amakuvutitsani,+ adzaweruzidwa+ kaya akhale ndani. 11 Kunena za ine abale, ngati ndimalalikirabe kuti anthu azidulidwa, n’chifukwa chiyani ndikuzunzidwabe? Ndithudi, mtengo wozunzikirapo,+ womwe ndi chopunthwitsa,+ ukanakhala utachotsedwa.+ 12 Ndikanakonda kuti anthu amene akufuna kukupotozani maganizo,+ afulidwe.+
13 Zoonadi abale, munaitanidwa kuti mukhale aufulu,+ musayese ngakhale pang’ono kugwiritsa ntchito ufulu umenewu polimbikitsira zilakolako za thupi,+ koma tumikiranani mwachikondi.+ 14 Pakuti Chilamulo chonse chimakwaniritsidwa+ m’mawu akuti: “Uzikonda mnzako ngati mmene umadzikondera wekha.”+ 15 Koma mukamalumana ndi kudyana nokhanokha,+ chenjerani kuti mungawonongane.+
16 M’malomwake ndikuti, Pitirizani kuyenda mwa mzimu,+ ndipo simudzatsatira chilakolako cha thupi ngakhale pang’ono.+ 17 Pakuti zilakolako za thupi zimalimbana ndi mzimu,+ mzimunso umalimbana ndi thupi. Zinthu ziwiri zimenezi zimatsutsana, choncho zinthu zimene mumafuna kuchita simuzichita.+ 18 Komanso ngati mukutsogoleredwa ndi mzimu,+ simuli pansi pa chilamulo.+
19 Tsopano, ntchito za thupi zimaonekera.+ Ntchitozi ndizo dama,*+ zinthu zodetsa, khalidwe lotayirira,+ 20 kupembedza mafano, kuchita zamizimu,+ udani, ndewu, nsanje, kupsa mtima, mikangano, kugawikana, magulu ampatuko, 21 kaduka, kumwa mwauchidakwa,*+ maphwando aphokoso, ndi zina zotero. Ponena za zinthu zimenezi, ndikukuchenjezeranitu, ngati mmene ndinachitira poyamba paja, kuti anthu amene amachita zimenezi+ sadzalowa mu ufumu wa Mulungu.+
22 Koma makhalidwe* amene mzimu woyera umatulutsa+ ndiwo chikondi, chimwemwe, mtendere, kuleza mtima, kukoma mtima, ubwino,+ chikhulupiriro, 23 kufatsa ndi kudziletsa.+ Palibe lamulo loletsa zinthu zoterezi.+ 24 Ndiponso anthu amene ali a Khristu Yesu, anapachika thupi lawo pamodzi ndi zikhumbo zake ndi zilakolako zake.+
25 Ngati tikukhala mwa mzimu, tiyeninso tipitirize kuyenda motsogoleredwa ndi mzimuwo.+ 26 Tisakhale odzikuza, oyambitsa mpikisano+ pakati pathu, ndi ochitirana kaduka.+