Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • Oweruza 6:31
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 31 Koma Yowasi+ anauza onse amene anamuukirawo kuti:+ “Kodi inu mungaweruzire Baala mlandu kuti mum’pulumutse? Aliyense womuweruzira mlandu ayenera kuphedwa m’mawa womwe uno.+ Ngati Baalayo ndi Mulungu,+ adziweruzire yekha mlanduwu,+ chifukwa wina wake wagwetsa guwa lake lansembe.”

  • 1 Samueli 24:15
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 15 Yehova akhale woweruza, ndipo aweruze pakati pa ine ndi inu. Iye adzandiweruzira mlanduwu+ ndi kuchitapo kanthu kuti andimasule m’manja mwanu.”

  • Salimo 35:1
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 35 Weruzani mlandu wanga inu Yehova, motsutsana ndi adani anga.+

      Menyani nkhondo ndi kugonjetsa amene akumenyana ndi ine.+

  • Salimo 43:1
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 43 Ndiweruzeni+ inu Mulungu,

      Weruzani mlandu wanga+ motsutsana ndi mtundu wosakhulupirika.

      Ndipulumutseni kwa munthu wachinyengo ndi wochita zosalungama.+

  • Miyambo 22:23
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 23 Pakuti Yehova adzawateteza pa mlandu wawo,+ ndipo adzalanda moyo wa amene akuwabera.+

  • Miyambo 23:11
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 11 Pakuti Wowawombola ndi wamphamvu, ndipo adzawateteza pa mlandu wawo ndi iwe.+

  • Yeremiya 50:34
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 34 Wowawombola ndi wamphamvu,+ dzina lake ndi Yehova wa makamu.+ Iye sadzalephera kuwaweruzira mlandu wawo+ kuti apumitse dziko lawo+ ndiponso kusokoneza mtendere wa anthu okhala m’Babulo.”+

  • Maliro 3:59
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 59 Inu Yehova, mwaona zoipa zimene andichitira.+ Chonde, ndiweruzireni mlandu wanga.+

  • Mika 7:9
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 9 Mkwiyo waukulu wa Yehova ndiupirira chifukwa ndamuchimwira.+ Ndiupirirabe kufikira ataweruza mlandu wanga mondikomera ndi kundichitira chilungamo.+ Iye adzandipititsa pamalo owala ndipo ndidzaona kulungama kwake.+

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena