Miyambo
3 Mwana wanga, usaiwale lamulo langa,+ ndipo mtima wako usunge malamulo anga.+ 2 Ukatero, udzakhala ndi masiku ochuluka, moyo wazaka zambiri,+ ndi mtendere.+ 3 Usasiye kukoma mtima kosatha ndi choonadi.+ Uzimange m’khosi mwako+ ndiponso uzilembe pamtima pako.+ 4 Ukachita zimenezi, Mulungu ndi anthu adzakukomera mtima ndipo adzakuona kuti ndiwe wozindikira.+ 5 Khulupirira Yehova ndi mtima wako wonse,+ ndipo usadalire luso lako lomvetsa zinthu.+ 6 Uzim’kumbukira m’njira zako zonse,+ ndipo iye adzawongola njira zako.+
7 Usamadzione kuti ndiwe wanzeru.+ Uziopa Yehova ndi kupatuka pa choipa.+ 8 Zimenezi zidzachiritsa+ mchombo wako ndi kutsitsimutsa mafupa ako.+
9 Uzilemekeza Yehova ndi zinthu zako zamtengo wapatali+ ndiponso ndi zipatso zako zonse zoyambirira.+ 10 Ukatero nkhokwe zako zidzakhala zodzaza+ ndipo zoponderamo mphesa zako zidzasefukira ndi vinyo watsopano.+
11 Mwana wanga, usakane malangizo* a Yehova+ ndipo usanyansidwe ndi kudzudzula kwake,+ 12 chifukwa Yehova amadzudzula munthu amene amam’konda,+ monga momwe bambo amadzudzulira mwana amene amakondwera naye.+
13 Wodala ndi munthu amene wapeza nzeru,+ ndiponso munthu amene wapeza kuzindikira,+ 14 chifukwa kupeza nzeru monga phindu n’kwabwino kuposa kupeza siliva monga phindu, ndipo kukhala nazo monga zokolola n’kwabwino kuposa kukhala ndi golide.+ 15 N’zamtengo wapatali kuposa miyala ya korali,+ ndipo zonse zimene umakonda sizingafanane nazo. 16 Masiku ochuluka ali m’dzanja lake lamanja.+ M’dzanja lake lamanzere muli chuma ndi ulemerero.+ 17 Njira zake n’zobweretsa chisangalalo ndipo misewu yake yonse ndi yamtendere.+ 18 Munthu akagwiritsitsa nzeru, zidzakhala ngati mtengo wa moyo+ kwa iye, ndipo ozigwiritsitsa+ adzatchedwa odala.+
19 Yehova anayala maziko a dziko lapansi mwanzeru.+ Anakhazikitsa kumwamba mozindikira.+ 20 Chifukwa chakuti iye amadziwa zinthu, anagawa madzi akuya,+ ndipo kumwamba kwa mitambo kumagwetsa mvula yamawawa.+ 21 Mwana wanga, zimenezi zisachoke pamaso pako.+ Usunge nzeru zopindulitsa ndiponso kuganiza bwino,+ 22 ndipo zidzatanthauza moyo kwa iwe+ komanso zidzakhala chokongoletsa m’khosi mwako.+ 23 Ukatero udzayenda panjira yako popanda chokuopseza,+ ndipo ngakhale phazi lako silidzapunthwa ndi chilichonse.+ 24 Nthawi iliyonse ukagona sudzaopa chilichonse.+ Udzagona ndithu, ndipo tulo tako tidzakhala tokoma.+ 25 Sudzaopa zoopsa zilizonse zadzidzidzi,+ kapena mphepo yamkuntho yowomba oipa, chifukwa ikubwera.+ 26 Pakuti Yehova ndiye amene uzidzamudalira,+ ndipo adzateteza phazi lako kuti lisakodwe.+
27 Usalephere kuchitira zabwino anthu amene akufunikira zabwinozo,+ pamene dzanja lako lingathe kuchita zimenezo.+ 28 Usanene kwa mnzako kuti, “Pita, ukabwerenso mawa ndidzakupatsa,” pamene uli ndi chinachake choti ungam’patse.+ 29 Usakonze zochitira mnzako choipa,+ pamene iye akuona kuti akukhala nawe mwamtendere.+ 30 Usakangane ndi munthu popanda chifukwa,+ ngati sanakuchitire choipa.+
31 Usasirire munthu wachiwawa,+ kapena kusankha njira zake.+ 32 Pakuti munthu wochita zachiphamaso+ Yehova amanyansidwa naye,+ koma amakonda anthu owongoka mtima.+ 33 Temberero la Yehova lili panyumba ya munthu woipa,+ koma malo okhala anthu olungama, iye amawadalitsa.+ 34 Onyoza,+ iye amawanyoza,+ koma ofatsa amawakomera mtima.+ 35 Anzeru adzapeza ulemu,+ koma opusa amatama zinthu zimene zidzawachititse manyazi.+