Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • nwt 2 Timothy 1:1-4:22
  • 2 Timoteyo

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • 2 Timoteyo
  • Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
2 Timoteyo

KALATA YACHIWIRI YOPITA KWA TIMOTEYO

1 Ine Paulo, mtumwi wa Khristu Yesu mwakufuna kwa Mulungu, mogwirizana ndi lonjezo la moyo umene tingapeze chifukwa chokhala otsatira a Khristu Yesu,+ 2 ndikulembera iwe Timoteyo mwana wanga wokondedwa:+

Kukoma mtima kwakukulu, chifundo ndi mtendere zochokera kwa Atate wathu Mulungu, ndi kwa Khristu Yesu Ambuye wathu, zikhale nawe.

3 Ndikuthokoza Mulungu amene ndikumuchitira utumiki wopatulika ngati mmene makolo anga akale anachitira. Ndikuuchita ndi chikumbumtima choyera ndipo sindiiwala kukutchula mʼmapemphero anga opembedzera, usana ndi usiku. 4 Ndikakumbukira misozi yako ndimalakalaka kukuona kuti ndidzasangalale kwambiri. 5 Chifukwa ndikukumbukira chikhulupiriro chako chopanda chinyengo,+ chimene anayamba kukhala nacho ndi agogo ako aakazi a Loisi komanso amayi ako a Yunike, ndipo ndikukhulupirira kuti iwenso uli nacho.

6 Chifukwa cha zimenezi, ndikukukumbutsa kuti mphatso ya Mulungu imene uli nayo, yomwe unailandira pamene ndinaika manja pa iwe,+ uikolezere ngati moto. 7 Chifukwatu Mulungu sanatipatse mzimu wamantha,+ koma wamphamvu,+ wachikondi ndi woti tiziganiza bwino. 8 Choncho usachite manyazi ndi ntchito yolalikira za Ambuye wathu,+ kapena kuchita manyazi ndi ineyo amene ndine mkaidi chifukwa cha iye. Koma khala wokonzeka kuvutika+ chifukwa cha uthenga wabwino ndipo uzidalira mphamvu ya Mulungu.+ 9 Iye anatipulumutsa ndiponso anatiitana kuti tikhale oyera,+ osati chifukwa cha ntchito zathu, koma chifukwa cha cholinga chake ndi kukoma mtima kwake kwakukulu.+ Mulungu anatisonyeza kukoma mtimaku kalekale chifukwa cha Khristu Yesu. 10 Koma tsopano izi zatsimikizirika chifukwa cha kuonekera kwa Mpulumutsi wathu Khristu Yesu,+ amene wathetsa mphamvu za imfa.+ Komanso pogwiritsa ntchito uthenga wabwino,+ watidziwitsa mmene tingapezere moyo+ wosawonongeka.+ 11 Ndipo ndinasankhidwa kuti ndikhale mlaliki, mtumwi ndi mphunzitsi+ wa uthenga wabwinowu.

12 Nʼchifukwa chake ndikuvutika chonchi,+ koma sindikuchita manyazi.+ Ndikudziwa amene ndikumukhulupirira, ndipo sindikukayikira kuti adzateteza zonse zimene ndamupatsa mpaka tsiku lachiweruzo.+ 13 Gwiritsitsabe chitsanzo cha mawu olondola+ amene unawamva kwa ine pamene ukusonyeza chikhulupiriro ndi chikondi zomwe timakhala nazo chifukwa chogwirizana ndi Khristu Yesu. 14 Usunge chuma chapadera chimene unapatsidwachi. Uchisunge mothandizidwa ndi mzimu woyera umene tili nawo.+

15 Iwe ukudziwa kuti anthu onse mʼchigawo cha Asia+ andisiya. Ena mwa anthuwa ndi Fugelo ndi Heremogene. 16 Ambuye achitire chifundo banja la Onesiforo,+ chifukwa ankabwera kawirikawiri kudzandilimbikitsa, ndipo sanachite manyazi ndi maunyolo anga. 17 Moti pamene anali ku Roma, anandifunafuna mwakhama mpaka anandipeza. 18 Ambuye Yehova* adzamuchitire chifundo pa tsiku lachiweruzo. Iwe ukudziwa bwino za utumiki wonse umene anachita ku Efeso.

2 Choncho iwe mwana wanga,+ pitiriza kupeza mphamvu mʼkukoma mtima kwakukulu kwa Khristu Yesu. 2 Zinthu zimene unazimva kwa ine ndi kwa mboni zambiri,+ uziphunzitse kwa anthu okhulupirika ndipo nawonso adzakhala oyenerera kuphunzitsa ena. 3 Monga msilikali wabwino+ wa Khristu Yesu, khala wokonzeka kukumana ndi mavuto.+ 4 Msilikali sachita nawo* zamalonda* zimene anthu ena amachita, pofuna kukondweretsa amene anamulemba usilikali. 5 Ngakhalenso pa mpikisano, munthu salandira mphoto* akapanda kupikisana nawo motsatira malamulo.+ 6 Mlimi wakhama ayenera kukhala woyambirira kudya zipatso za mbewu zake. 7 Nthawi zonse uziganizira zimene ndikukuuzazi ndipo Ambuye adzakuthandiza kumvetsa zinthu zonse.

8 Kumbukira kuti, mogwirizana ndi uthenga wabwino umene ndikulalikira,+ Yesu Khristu anaukitsidwa+ ndipo anali mbadwa ya Davide.+ 9 Chifukwa cha uthengawu, ndikuvutika ndipo ndatsekeredwa mʼndende ngati chigawenga.+ Komabe mawu a Mulungu samangika.+ 10 Choncho ndikupirirabe zinthu zonse chifukwa cha anthu osankhidwa,+ kuti nawonso alandire chipulumutso kudzera mwa Khristu Yesu komanso alandire ulemerero wosatha. 11 Mawu awa ndi oona: Ndithudi, ngati tinafa naye limodzi, tidzakhalanso ndi moyo limodzi naye.+ 12 Tikapitiriza kupirira, tidzalamuliranso naye monga mafumu.+ Tikamukana, iyenso adzatikana,+ 13 koma tikakhala osakhulupirika, iye adzakhalabe wokhulupirika, chifukwa sangadzikane.

14 Uziwakumbutsa zimenezi nthawi zonse. Uziwalangiza* pamaso pa Mulungu, kuti asamakangane pa mawu. Kuchita zimenezi kulibe phindu mʼpangʼono pomwe chifukwa kumawononga chikhulupiriro cha omvetsera. 15 Chita chilichonse chotheka kuti usonyeze kuti ndiwe wovomerezeka pamaso pa Mulungu, munthu wosachita manyazi ndi ntchito imene wagwira ndiponso wophunzitsa ndi kufotokoza bwino mawu a choonadi.+ 16 Koma uzipewa nkhani zopeka zimene zimaipitsa zinthu zoyera+ chifukwa zimachititsa kuti anthu ambiri asamaope Mulungu, 17 ndipo mawu awo amafalikira ngati chilonda chonyeka. Ena mwa anthu amenewo ndi Hemenayo ndi Fileto.+ 18 Anthu amenewa akupotoza choonadi, ponena kuti akufa anauka kale+ ndipo akuwononga chikhulupiriro cha ena. 19 Komabe, maziko olimba a Mulungu adakalipo, ndipo ali ndi chidindo cha mawu akuti: “Yehova* amadziwa anthu ake,”+ ndiponso akuti: “Aliyense woitana pa dzina la Yehova*+ aleke kuchita zosalungama.”

20 Mʼnyumba yaikulu simukhala zinthu* zagolide ndi zasiliva zokha, koma mumakhalanso zamtengo ndi zadothi. Zinthu zina zimakhala za ntchito yolemekezeka, koma zina zimakhala za ntchito yonyozeka. 21 Choncho ngati munthu akupewa zinthu za ntchito yonyozekazo, adzakhala chinthu* cha ntchito yolemekezeka, choyera, chofunika kwa mwiniwake, ndi chokonzeka kugwira ntchito iliyonse yabwino. 22 Choncho thawa zilakolako za unyamata, koma tsatira chilungamo, chikhulupiriro, chikondi ndi mtendere limodzi ndi anthu oitana pa Ambuye ndi mtima woyera.

23 Ndiponso, uzipewa kutsutsana pa zinthu zopusa ndi zopanda nzeru+ chifukwa zimayambitsa mikangano. 24 Kapolo wa Ambuye sayenera kukangana ndi anthu. Koma ayenera kukhala wodekha kwa onse,+ woyenerera kuphunzitsa, wougwira mtima ena akamulakwira+ 25 ndiponso wotha kulangiza mofatsa anthu otsutsa+ kuti mwina Mulungu angawalole kulapa* nʼkudziwa choonadi molondola.+ 26 Komanso mwina nzeru zingawabwerere nʼkupulumuka mumsampha wa Mdyerekezi, chifukwa wawagwira amoyo pofuna kuti azichita zofuna zake.+

3 Koma dziwa kuti masiku otsiriza+ adzakhala nthawi yapadera komanso yovuta. 2 Anthu adzakhala odzikonda, okonda ndalama, odzitama, odzikweza, onyoza, osamvera makolo, osayamika, osakhulupirika, 3 osakonda achibale awo, osafuna kugwirizana ndi ena, onenera ena zoipa, osadziletsa, oopsa, osakonda zabwino, 4 ochitira anzawo zoipa, osamva za ena, odzitukumula chifukwa cha kunyada, okonda zosangalatsa mʼmalo mokonda Mulungu, 5 ndiponso ooneka ngati odzipereka kwa Mulungu koma amakana kuti mphamvu ya kudziperekako iwasinthe.+ Anthu amenewa uziwapewa. 6 Ena mwa anthuwa amalowerera mozemba mʼmabanja nʼkumachititsa amayi ena kuti akhale akapolo awo. Amayiwa amakhala ofooka chifukwa cha machimo awo ndiponso otengeka ndi zilakolako zosiyanasiyana. 7 Nthawi zonse amaphunzira, koma satha kudziwa choonadi molondola.

8 Mofanana ndi Yane ndi Yambure, amene anatsutsa Mose, anthu amenewanso akupitiriza kutsutsa choonadi. Iwo ali ndi maganizo opotoka kwambiri, ndipo sakuyenerera chikhulupirirochi. 9 Koma sangapite patali, chifukwa kupusa kwawo kuonekera bwino kwa anthu onse, ngati mmene zinakhalira ndi anthu awiri aja.+ 10 Koma iwe wayesetsa kutsatira zimene ndimaphunzitsa, moyo wanga,+ cholinga changa, chikhulupiriro changa, kuleza mtima kwanga, chikondi changa ndi kupirira kwanga. 11 Ukudziwanso mmene ndinazunzikira komanso masautso amene ndinakumana nawo ku Antiokeya,+ ku Ikoniyo+ ndi ku Lusitara.+ Komabe ndinapirira ndipo Ambuye anandipulumutsa ku zonsezi.+ 12 Pajatu onse ofuna kukhala ndi moyo wodzipereka kwa Mulungu mogwirizana ndi Khristu Yesu, nawonso adzazunzidwa.+ 13 Koma anthu oipa ndi achinyengo adzaipiraipirabe. Iwo azidzasocheretsa ena ndiponso azidzasocheretsedwa.+

14 Koma iwe, pitiriza kutsatira zimene unaphunzira ndi zimene unakhulupirira pambuyo pokhutira nazo,+ chifukwa ukudziwa amene anakuphunzitsa. 15 Kuyambira pamene unali wakhanda,+ wadziwa malemba oyera+ amene angakupatse nzeru zokuthandiza kuti udzapulumuke chifukwa chokhulupirira Khristu Yesu.+ 16 Malemba onse anauziridwa ndi Mulungu,+ ndipo ndi othandiza pophunzitsa,+ kudzudzula, kukonza zinthu ndi kulangiza mwachilungamo,+ 17 kuti munthu wa Mulungu akhale woyenerera kwambiri ndi wokonzeka mokwanira kugwira ntchito iliyonse yabwino.

4 Pamaso pa Mulungu ndi Khristu Yesu, amene adzaweruze+ amoyo ndi akufa,+ akadzaonekera+ ndiponso akadzabwera mu Ufumu wake,+ ndikukulamula mwamphamvu kuti: 2 Lalikira mawu.+ Uzilalikira modzipereka, pa nthawi yabwino ndi pa nthawi yovuta. Dzudzula,+ tsutsa, dandaulira, ndipo uzichita zimenezi ndi luso la kuphunzitsa+ ndiponso moleza mtima kwambiri. 3 Chifukwa idzafika nthawi imene anthu sadzafunanso kuphunzitsidwa zolondola,+ koma mogwirizana ndi zimene amalakalaka, adzapeza aphunzitsi oti aziwauza zowakomera mʼkhutu.+ 4 Iwo adzasiya kumvetsera choonadi nʼkumamvetsera nkhani zonama. 5 Koma iwe ukhalebe woganiza bwino pa zinthu zonse, uzipirira mavuto,+ uzigwira ntchito ya mlaliki* ndiponso uzikwaniritsa mbali zonse za utumiki wako.+

6 Ndili ngati nsembe yachakumwa imene ikuthiridwa paguwa la nsembe,+ ndipo nthawi yoti ndimasuke+ yatsala pangʼono. 7 Ndamenya nkhondo yabwino.+ Ndathamanga pa mpikisanowu mpaka pamapeto.+ Ndakhalabe ndi chikhulupiriro. 8 Panopa andisungira chisoti chachifumu cha olungama.+ Ambuye, woweruza wachilungamo,+ adzandipatsa mphotoyi pa tsikulo.+ Sikuti adzapatsa ine ndekha, koma adzapatsanso onse amene akhala akuyembekezera kuti iye adzaonekere.

9 Yesetsa kuti ubwere posachedwapa. 10 Kuno Dema+ wandisiya chifukwa chokonda zinthu zamʼdzikoli* ndipo wapita ku Tesalonika. Keresike wapita ku Galatiya ndipo Tito wapita ku Dalimatiya. 11 Luka yekha ndi amene watsala. Ubwerenso ndi Maliko chifukwa amandithandiza pa utumiki wanga. 12 Koma Tukiko+ ndamutuma ku Efeso. 13 Ukamabwera unditengerekonso chovala champhepo chimene ndinachisiya ku Torowa kwa Karipo komanso mipukutu, makamaka yazikopa ija.

14 Alekizanda wosula zinthu zakopa uja, anandichitira zoipa kwambiri. Yehova* adzamubwezera mogwirizana ndi ntchito zake.+ 15 Iwenso uchenjere naye, chifukwa anatsutsa uthenga wathu mwamphamvu.

16 Pamene ndinkadziteteza koyamba pa mlandu wanga palibe anakhala kumbali yanga, moti onse anandisiya. Komabe asakhale ndi mlandu. 17 Koma Ambuye anaima nane pafupi nʼkundipatsa mphamvu. Anachita zimenezi kuti kudzera mwa ine, ntchito yolalikira ichitike mokwanira, ndi kuti mitundu yonse ya anthu imve uthengawo.+ Ndiponso ndinapulumutsidwa mʼkamwa mwa mkango.+ 18 Ambuye adzandipulumutsa ku choipa chilichonse ndipo adzandisunga kuti ndikakhale mu Ufumu wake wakumwamba.+ Iye apatsidwe ulemerero mpaka muyaya. Ame.

19 Undiperekere moni kwa Purisika ndi Akula+ komanso banja la Onesiforo.+

20 Erasito+ anatsala ku Korinto, koma Terofimo+ ndinamusiya akudwala ku Mileto. 21 Uyesetse kuti ufike kuno nyengo yozizira isanayambe.

Ebulo, Pude, Lino, Kalaudiya komanso abale onse akupereka moni.

22 Ambuye akhale nawe chifukwa cha mzimu umene umasonyeza. Kukoma mtima kwake kwakukulu kukhale nanu.

Onani Zakumapeto A5.

Kapena kuti, “sasokonezedwa ndi.”

Mabaibulo ena amati, “zochita za tsiku ndi tsiku.”

Kapena kuti, “nkhata yosonyeza kuti wapambana.”

Mʼchilankhulo choyambirira, “Uzichitira umboni mokwanira.”

Onani Zakumapeto A5.

Onani Zakumapeto A5.

Kapena kuti, “ziwiya.”

Kapena kuti, “chiwiya.”

Kapena kuti, “kusintha maganizo.”

Kapena kuti, “yolalikira uthenga wabwino.”

Kapena kuti, “za mʼnthawi ino.” Onani Matanthauzo a Mawu Ena.

Onani Zakumapeto A5.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena