Yobu
20 Tsopano Zofari wa ku Naama anayankha kuti:
2 “N’chifukwa chake malingaliro anga osautsa akundiyankha,
Chifukwa cha mkwiyo wa mumtima mwanga.
3 Ndikumva mawu ondinyoza,
Ndipo munthu wa mtima wopanda nzeru ngati zimene ine ndili nazo, akundiyankha.
4 Kodi wakhala ukudziwa zimenezi kuyambira kalekale,
Kuyambira pamene munthu anaikidwa padziko lapansi?+
5 Kuti mfuu yachisangalalo ya anthu oipa sikhalitsa,+
Ndiponso kuti kusangalala kwa wampatuko kumakhala kwa kanthawi?
6 Ngakhale kuti ulemerero wake umafika mpaka kumwamba,+
Ndipo mutu wake umafika m’mitambo?
7 Adzatheratu mofanana ndi ndowe zake.+
Amene ankamuona adzati, ‘Ali kuti kodi?’+
10 Ana ake adzafunafuna kuti anthu onyozeka awachitire chifundo.
Manja ake adzabweza zinthu zake zamtengo wapatali.+
12 Ngati zoipa zimatsekemera* m’kamwa mwake,
Ngati amazibulumunya kuseri kwa lilime lake,
13 Ngati amazikonda ndipo sazisiya,
Ngati amazivumata m’kamwa mwake,
14 Chakudya chake chidzasintha m’matumbo mwake.
Chidzakhala poizoni wa mamba m’thupi mwake.
15 Wameza chuma, koma adzachisanza.
Mulungu adzachithamangitsa m’mimba mwake.
18 Adzabweza chuma chimene anachipeza ndipo sadzachimeza.
Chumacho chidzakhala ngati chuma chochokera ku malonda ake chimene sadzachidyerera.+
21 Palibe chimene chatsala choti ameze,
N’chifukwa chake ulemerero wake sudzakhalitsa.
23 Mulungu atumize mkwiyo wake woyaka moto pa iye,
N’kuudzaza m’mimba mwake.+
Auvumbitsire pa iye kuti ufike mpaka m’matumbo mwake.
25 Muvi udzatulukira kumsana kwake,
Ndipo chida chonyezimira chidzaboola ndulu yake.+
Zida zoopsa zidzam’pweteka.+
26 Zinthu zake zapamtima zidzakumana ndi mdima wokhawokha.
Moto wopanda woukolezera udzamunyeketsa.+
Munthu wotsala muhema wake zinthu zidzamuipira.