12 Mana analeka kugwa pa tsikuli, pamene ana a Isiraeli anadya zokolola za m’dzikomo. Kuyambira pamenepo, mana sanagwenso pakati pa ana a Isiraeli.+ Chotero, chaka chimenechi n’chimene iwo anayamba kudya zokolola za m’dziko la Kanani.+
58 Chimenechi ndiye chakudya chotsika kumwamba. N’chosiyana ndi chakudya chimene makolo anu anadya koma anamwalirabe. Iye wakudya chakudya ichi adzakhala ndi moyo kosatha.”+