6 Yehova Mulungu wanu adzachita mdulidwe wa mitima yanu+ ndi mitima ya ana anu,+ kuti muzikonda Yehova Mulungu wanu ndi mtima wanu wonse ndi moyo wanu wonse, kuti mukhale ndi moyo.+
4 Chitani mdulidwe wa mitima yanu pamaso pa Yehova,+ inu anthu a ku Yuda ndi okhala mu Yerusalemu. Chitani zimenezi kuti mkwiyo wanga usayake ngati moto, pakuti ukatero udzayaka popanda munthu wozimitsa, chifukwa cha zochita zanu zoipa.”+
26 Ndidzaimba mlandu Iguputo,+ Yuda,+ Edomu,+ ana aamuna a Amoni+ ndi Mowabu+ ndi onse odulira ndevu zawo zam’mbali amene amakhala m’chipululu.+ Pakuti mitundu yonse ndi yosadulidwa ndipo anthu onse a m’nyumba ya Isiraeli sanachite mdulidwe wa mitima yawo.”+
51 “Anthu okanika inu ndi osachita mdulidwe wa mumtima+ ndi m’makutu. Nthawi zonse mumatsutsana ndi mzimu woyera. Mmene anachitira makolo anu inunso mukuchita chimodzimodzi.+
29 Koma Myuda ndi amene ali wotero mkati,+ ndipo mdulidwe wake ndi wa mumtima+ wochitidwa ndi mzimu, osati ndi malamulo olembedwa.+ Munthu woteroyo satamandidwa+ ndi anthu koma ndi Mulungu.+