5 Choncho Yetero, apongozi ake a Mose, pamodzi ndi ana a Mose awiri aamuna ndi mkazi wake, anapita kwa Mose kuchipululu, kuphiri la Mulungu woona, kumene anamanga msasa.+
1Yehova anapitiriza kulankhula ndi Mose m’chipululu cha Sinai,+ m’chihema chokumanako.+ Analankhula naye pa tsiku loyamba la mwezi wachiwiri m’chaka chachiwiri, atatuluka m’dziko la Iguputo.+ Iye anati: