Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • Deuteronomo 15:10
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 10 Mulimonse mmene zingakhalire uzim’patsa zimene akufunazo,+ ndipo mtima wako usakhale woumira pomupatsa zinthu zimenezo, chifukwa ukakhala wowolowa manja, Yehova Mulungu wako adzakudalitsa pa chilichonse chimene ukuchita ndi pa ntchito zako zonse.+

  • Miyambo 11:24
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 24 Pali amene amapatsa mowolowa manja, komabe zinthu zake zimawonjezeka.+ Palinso amene safuna kupatsa ena zinthu zoyenera kuwapatsa, koma amangokhala wosowa.+

  • Miyambo 14:21
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 21 Munthu wonyoza mnzake ndiye kuti akuchimwa,+ koma wodala ndi munthu wokomera mtima anthu osautsika.+

  • Miyambo 19:17
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 17 Wokomera mtima munthu wonyozeka akukongoza Yehova,+ ndipo adzam’bwezera zimene anachitazo.+

  • Luka 6:38
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 38 Khalani opatsa ndipo inunso anthu adzakupatsani.+ Adzakhuthulira m’matumba anu muyezo wabwino, wotsendereka, wokhutchumuka ndi wosefukira. Pakuti muyezo umene mukuyezera ena, iwonso adzakuyezerani womwewo.”+

  • 2 Akorinto 9:6
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 6 Koma ponena za nkhaniyi, wobzala moumira+ adzakololanso zochepa, ndipo wobzala mowolowa manja+ adzakololanso zochuluka.

  • 1 Yohane 3:17
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 17 Koma aliyense amene ali ndi zinthu zofunika pa moyo,+ n’kuona m’bale wake zikumusowa,+ koma osamusonyeza m’bale wakeyo chifundo chachikulu,+ kodi munthu ameneyu amakonda Mulungu?+

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena