Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • Deuteronomo 4:6
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 6 Ndipo muyenera kusunga malangizo ndi zigamulo zimenezi, chifukwa mukatero mudzakhala anzeru+ ndi ozindikira+ pamaso pa anthu a mitundu ina amene adzamva za malangizo onsewa. Pamenepo, anthuwo adzanena kuti, ‘Mtundu waukulu umenewu ndi wa anthu anzerudi ndi ozindikira.’+

  • Deuteronomo 8:18
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 18 Muzikumbukira Yehova Mulungu wanu, chifukwa ndiye amakupatsani mphamvu kuti mupeze chuma,+ pofuna kusunga pangano lake limene analumbirira makolo anu, monga mmene wachitira lero.+

  • Yoswa 1:7
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 7 “Iwe khala wolimba mtima kwambiri ndipo uchite zinthu mwamphamvu. Uonetsetse kuti ukutsatira malamulo onse amene mtumiki wanga Mose anakulamula.+ Malamulowo usawasiye ndi kupatukira kudzanja lamanja kapena lamanzere,+ kuti uchite mwanzeru kulikonse kumene udzapitako.+

  • 1 Mafumu 2:3
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 3 Uzimvera Yehova Mulungu wako mwa kuyenda m’njira zake,+ kusunga malamulo ake, zigamulo zake,+ ndi maumboni* ake, malinga ndi zimene zinalembedwa m’chilamulo cha Mose.+ Uzitero kuti udzakhale wanzeru m’zochita zako zonse, ndiponso kulikonse kumene udzapite.

  • Salimo 103:17
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 17 Koma Yehova adzapitiriza kusonyeza kukoma mtima kwake kosatha mpaka kalekale,+

      Kwa anthu amene amamuopa.+

      Ndipo adzapitiriza kusonyeza chilungamo chake kwa ana a ana awo.+

  • Salimo 103:18
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 18 Adzapitiriza kuchita zimenezi kwa anthu osunga pangano lake,+

      Ndi kwa anthu okumbukira malamulo ake ndi kuwatsatira.+

  • Luka 11:28
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 28 Koma iye anati: “Ayi, m’malomwake, Odala ndi amene akumva mawu a Mulungu ndi kuwasunga!”+

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena