Deuteronomo 29:9 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 9 Choncho muzisunga mawu a pangano ili kuti zonse zimene muzichita zizikuyenderani bwino.+ Salimo 1:2 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 2 Koma amakondwera ndi chilamulo cha Yehova,+Ndipo amawerenga ndi kusinkhasinkha chilamulo chake usana ndi usiku.+ Salimo 112:1 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 112 Tamandani Ya, anthu inu!+ א [ʼAʹleph]Wodala ndi munthu woopa Yehova,+ב [Behth]Munthu amene amasangalala kwambiri+ ndi malamulo ake.+ Salimo 119:2 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 2 Odala ndi anthu amene amasunga zikumbutso zake,+Amene amayesetsa kumufunafuna ndi mtima wonse.+ Yesaya 56:2 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 2 Wodala ndi munthu amene amachita zimenezi,+ ndiponso mwana wa munthu amene amatsatira zimenezi,+ amene amasunga sabata kuti asalidetse,+ ndiponso amaletsa dzanja lake kuti lisachite choipa chilichonse.+ Mateyu 7:21 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 21 “Sikuti aliyense wonena kwa ine kuti, ‘Ambuye, Ambuye,’ adzalowa ufumu wakumwamba ayi, koma yekhayo amene akuchita+ chifuniro cha Atate wanga wakumwamba.+ Yakobo 1:25 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 25 Koma woyang’anitsitsa m’lamulo langwiro+ limene limabweretsa ufulu, amene amalimbikira kutero, adzakhala wosangalala+ polichita chifukwa chakuti sali wongomva n’kuiwala, koma wochita.+
2 Koma amakondwera ndi chilamulo cha Yehova,+Ndipo amawerenga ndi kusinkhasinkha chilamulo chake usana ndi usiku.+
112 Tamandani Ya, anthu inu!+ א [ʼAʹleph]Wodala ndi munthu woopa Yehova,+ב [Behth]Munthu amene amasangalala kwambiri+ ndi malamulo ake.+
2 Wodala ndi munthu amene amachita zimenezi,+ ndiponso mwana wa munthu amene amatsatira zimenezi,+ amene amasunga sabata kuti asalidetse,+ ndiponso amaletsa dzanja lake kuti lisachite choipa chilichonse.+
21 “Sikuti aliyense wonena kwa ine kuti, ‘Ambuye, Ambuye,’ adzalowa ufumu wakumwamba ayi, koma yekhayo amene akuchita+ chifuniro cha Atate wanga wakumwamba.+
25 Koma woyang’anitsitsa m’lamulo langwiro+ limene limabweretsa ufulu, amene amalimbikira kutero, adzakhala wosangalala+ polichita chifukwa chakuti sali wongomva n’kuiwala, koma wochita.+