35 Choncho Aamori anakakamirabe kukhala m’phiri la Herese ndi m’mizinda ya Aijaloni+ ndi Saalibimu.+ Koma dzanja la nyumba ya Yosefe linakhala lamphamvu kwambiri, moti anayamba kugwiritsa ntchito yaukapolo Aamoriwo.+
13 Elipaala anaberekanso Beriya ndi Sema. Amenewa anali atsogoleri a nyumba za makolo a anthu okhala ku Aijaloni.+ Iwo ndiwo anathamangitsa anthu a ku Gati.
18 Nawonso Afilisiti+ anaukira mizinda ya Yuda ya ku Sefela+ ndi ku Negebu+ n’kulanda mizinda ya Beti-semesi,+ Aijaloni,+ Gederoti,+ Soko+ ndi midzi yake yozungulira, Timuna+ ndi midzi yake yozungulira, komanso Gimizo ndi midzi yake yozungulira, n’kuyamba kukhala kumeneko.