9 Zinthu zimenezi zitangotha, akalonga+ anabwera kwa ine n’kundiuza kuti: “Aisiraeli, ansembe ndiponso Alevi sanadzipatule+ kwa anthu a mitundu ina pa nkhani ya zinthu zonyansa+ za anthu a mitundu inawo. Anthu ake ndi Akanani,+ Ahiti,+ Aperezi,+ Ayebusi,+ Aamoni,+ Amowabu,+ Aiguputo+ ndi Aamori.+