Salimo 73:27 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 27 Pakuti onse okhala kutali ndi inu adzatheratu.+Mudzawononga ndithu aliyense wochita chigololo mwa kukusiyani.+ Yeremiya 3:8 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 8 Nditaona zimenezo, ndinam’pitikitsa+ ndipo ndinamupatsa kalata yotsimikizira kuti ukwati watha+ chifukwa chakuti Isiraeli wosakhulupirikayu anachita chigololo. Koma Yuda amene ndi m’bale wake wochita zachinyengo sanachite mantha ndipo nayenso anayamba kuchita uhule.+ Yeremiya 3:14 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 14 “Bwererani inu ana opanduka,”+ watero Yehova. “Ine ndakhala mwamuna wanu anthu inu.+ Ine ndidzakutengani, mmodzi kuchokera mumzinda uliwonse, awiri kuchokera mu fuko lililonse ndipo ndidzakupititsani ku Ziyoni.+ Ezekieli 23:3 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 3 Akazi amenewa anayamba kuchita uhule m’dziko la Iguputo.+ Anayamba uhule umenewu ali atsikana ang’onoang’ono.+ Kumeneko amuna anafinya mabere awo+ ndi kutsamira chifuwa chawo ali anamwali. Ezekieli 23:30 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 30 Adzakuchitira zimenezi chifukwa chakuti wachita uhule ndi mitundu ina ya anthu+ komanso chifukwa chakuti wadziipitsa ndi mafano awo onyansa.+ Yakobo 4:4 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 4 Achigololo+ inu, kodi simukudziwa kuti kuchita ubwenzi ndi dziko n’kudziika pa udani ndi Mulungu?+ Choncho, aliyense amene akufuna kukhala bwenzi+ la dziko akudzisandutsa mdani wa Mulungu.+
27 Pakuti onse okhala kutali ndi inu adzatheratu.+Mudzawononga ndithu aliyense wochita chigololo mwa kukusiyani.+
8 Nditaona zimenezo, ndinam’pitikitsa+ ndipo ndinamupatsa kalata yotsimikizira kuti ukwati watha+ chifukwa chakuti Isiraeli wosakhulupirikayu anachita chigololo. Koma Yuda amene ndi m’bale wake wochita zachinyengo sanachite mantha ndipo nayenso anayamba kuchita uhule.+
14 “Bwererani inu ana opanduka,”+ watero Yehova. “Ine ndakhala mwamuna wanu anthu inu.+ Ine ndidzakutengani, mmodzi kuchokera mumzinda uliwonse, awiri kuchokera mu fuko lililonse ndipo ndidzakupititsani ku Ziyoni.+
3 Akazi amenewa anayamba kuchita uhule m’dziko la Iguputo.+ Anayamba uhule umenewu ali atsikana ang’onoang’ono.+ Kumeneko amuna anafinya mabere awo+ ndi kutsamira chifuwa chawo ali anamwali.
30 Adzakuchitira zimenezi chifukwa chakuti wachita uhule ndi mitundu ina ya anthu+ komanso chifukwa chakuti wadziipitsa ndi mafano awo onyansa.+
4 Achigololo+ inu, kodi simukudziwa kuti kuchita ubwenzi ndi dziko n’kudziika pa udani ndi Mulungu?+ Choncho, aliyense amene akufuna kukhala bwenzi+ la dziko akudzisandutsa mdani wa Mulungu.+