2 Samueli 12:23 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 23 Koma tsopano popeza wamwalira, ndisale kudya chifukwa chiyani? Kodi ndingamuukitse?+ Inenso tsiku lina ndidzamwalira,+ koma iyeyo sangabwerere kwa ine.”+ Salimo 115:17 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 17 Akufa satamanda Ya,+Ngakhalenso aliyense wotsikira kuli chete.+ Salimo 146:4 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 4 Mzimu* wake umachoka,+ ndipo iye amabwerera kunthaka.+Pa tsiku limenelo zonse zimene anali kuganiza zimatheratu.+ Mlaliki 9:5 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 5 Pakuti amoyo amadziwa kuti adzafa,+ koma akufa sadziwa chilichonse.+ Iwo salandiranso malipiro alionse, chifukwa zonse zimene anthu akanawakumbukira nazo zaiwalika.+ Mlaliki 9:10 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 10 Chilichonse chimene dzanja lako lapeza kuti lichite, uchichite ndi mphamvu zako zonse,+ pakuti kulibe kugwira ntchito, kuganiza zochita, kudziwa zinthu,+ kapena nzeru,+ ku Manda*+ kumene ukupitako.+
23 Koma tsopano popeza wamwalira, ndisale kudya chifukwa chiyani? Kodi ndingamuukitse?+ Inenso tsiku lina ndidzamwalira,+ koma iyeyo sangabwerere kwa ine.”+
4 Mzimu* wake umachoka,+ ndipo iye amabwerera kunthaka.+Pa tsiku limenelo zonse zimene anali kuganiza zimatheratu.+
5 Pakuti amoyo amadziwa kuti adzafa,+ koma akufa sadziwa chilichonse.+ Iwo salandiranso malipiro alionse, chifukwa zonse zimene anthu akanawakumbukira nazo zaiwalika.+
10 Chilichonse chimene dzanja lako lapeza kuti lichite, uchichite ndi mphamvu zako zonse,+ pakuti kulibe kugwira ntchito, kuganiza zochita, kudziwa zinthu,+ kapena nzeru,+ ku Manda*+ kumene ukupitako.+