17 Ndiyeno zifanizo zagolide za matenda a mudzi zimene Afilisiti anapereka kwa Yehova monga nsembe ya kupalamula ndi izi:+ mzinda wa Asidodi+ unapereka chifanizo chimodzi, wa Gaza+ chimodzi, wa Asikeloni+ chimodzi, wa Gati+ chimodzi ndi wa Ekironi+ chimodzi.