Salimo 71:18 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 18 Ngakhale nditakalamba ndi kumera imvi, inu Mulungu musandisiye,+Kufikira nditanena za dzanja lanu lamphamvu ku m’badwo wotsatira,+Kufikira nditanena za mphamvu zanu kwa onse obwera m’tsogolo.+ Miyambo 16:31 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 31 Imvi ndizo chisoti chachifumu cha ulemerero+ zikapezeka m’njira yachilungamo.+ Miyambo 20:29 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 29 Kukongola kwa anyamata ndiko mphamvu zawo,+ ndipo ulemerero wa anthu okalamba ndiwo imvi zawo.+ Yesaya 46:4 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 4 Ine sindisintha ngakhale kwa wokalamba,+ ndipo munthu wa imvi ndimamunyamula nthawi zonse.+ Ndithu ineyo ndidzachitapo kanthu+ kuti ndiwatenge, ndiwanyamule ndi kuwapulumutsa.+
18 Ngakhale nditakalamba ndi kumera imvi, inu Mulungu musandisiye,+Kufikira nditanena za dzanja lanu lamphamvu ku m’badwo wotsatira,+Kufikira nditanena za mphamvu zanu kwa onse obwera m’tsogolo.+
4 Ine sindisintha ngakhale kwa wokalamba,+ ndipo munthu wa imvi ndimamunyamula nthawi zonse.+ Ndithu ineyo ndidzachitapo kanthu+ kuti ndiwatenge, ndiwanyamule ndi kuwapulumutsa.+