Genesis 39:9 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 9 M’nyumba muno mulibe woyang’anira woposa ine, ndipo mbuye wanga anaika chilichonse m’manja mwanga kupatulapo inuyo, chifukwa ndinu mkazi wake.+ Ndiye ndingachitirenji choipa chachikulu chonchi n’kuchimwira Mulungu?”+ Salimo 32:5 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 5 Pamapeto pake ndinaulula tchimo langa kwa inu, ndipo sindinabise cholakwa changa.+Ndinati: “Ndidzaulula kwa Yehova machimo anga.”+Ndipo inu munandikhululukira zolakwa zanga ndi machimo anga.+ [Seʹlah.] Salimo 38:3 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 3 Palibe pabwino m’thupi langa chifukwa cha chidzudzulo chanu.+Ndipo m’mafupa anga mulibe mtendere chifukwa cha tchimo langa.+ Salimo 51:4 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 4 Ine ndakuchimwirani kwambiri,+Ndipo ndachita chinthu choipa pamaso panu,+Choncho mukamalankhula mumalankhula zachilungamo,+Ndipo mukamaweruza, mumaweruza molungama.+ Miyambo 28:13 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 13 Wobisa machimo ake zinthu sizidzamuyendera bwino,+ koma woulula n’kuwasiya adzachitiridwa chifundo.+
9 M’nyumba muno mulibe woyang’anira woposa ine, ndipo mbuye wanga anaika chilichonse m’manja mwanga kupatulapo inuyo, chifukwa ndinu mkazi wake.+ Ndiye ndingachitirenji choipa chachikulu chonchi n’kuchimwira Mulungu?”+
5 Pamapeto pake ndinaulula tchimo langa kwa inu, ndipo sindinabise cholakwa changa.+Ndinati: “Ndidzaulula kwa Yehova machimo anga.”+Ndipo inu munandikhululukira zolakwa zanga ndi machimo anga.+ [Seʹlah.]
3 Palibe pabwino m’thupi langa chifukwa cha chidzudzulo chanu.+Ndipo m’mafupa anga mulibe mtendere chifukwa cha tchimo langa.+
4 Ine ndakuchimwirani kwambiri,+Ndipo ndachita chinthu choipa pamaso panu,+Choncho mukamalankhula mumalankhula zachilungamo,+Ndipo mukamaweruza, mumaweruza molungama.+
13 Wobisa machimo ake zinthu sizidzamuyendera bwino,+ koma woulula n’kuwasiya adzachitiridwa chifundo.+