Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • Genesis 34:7
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 7 Koma ana a Yakobo anabwerako kubusa kuja atangomva za nkhaniyi. Nkhaniyi inawapweteketsa mtima kwambiri ndipo anakwiya koopsa,+ pakuti Sekemu anachitira Isiraeli chinthu chonyazitsa kwambiri pogona ndi mwana wa Yakobo.+ Zimenezi zinali zosayenera kuchitika m’pang’ono pomwe.+

  • Levitiko 19:17
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 17 “‘Usadane ndi m’bale wako mumtima mwako.+ Mnzako um’dzudzule ndithu+ kuti usasenze naye tchimo.

  • Miyambo 18:19
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 19 M’bale amene walakwiridwa amaposa mzinda wolimba,+ ndipo pali mikangano imene imakhala ngati mtengo wotsekera pachipata cha nsanja yokhalamo.+

  • Miyambo 26:24
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 24 Munthu wodana nawe amadzibisa ndi milomo yake, koma mkati mwake mumakhala chinyengo.+

  • Aefeso 4:26
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 26 Kwiyani, koma musachimwe.+ Dzuwa lisalowe muli chikwiyire,+

  • 1 Yohane 3:15
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 15 Aliyense amene amadana+ ndi m’bale wake ndi wopha munthu,+ ndipo mukudziwa kuti aliyense wopha munthu+ sadzalandira moyo wosatha.+

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena