31 Koma Yehu sanayesetse kuyenda motsatira malamulo a Yehova Mulungu wa Isiraeli ndi mtima wake wonse.+ Sanapatuke pa machimo a Yerobowamu amene anachimwitsa nawo Isiraeli.+
2 Yehoahazi anapitiriza kuchita zoipa pamaso pa Yehova+ ndipo anayenda motsatira tchimo la Yerobowamu+ mwana wa Nebati, limene anachimwitsa nalo Isiraeli.+ Iye sanapatuke pa tchimolo.