Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • 1 Mafumu 17:24
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 24 Mayiyo ataona zimenezi anauza Eliya kuti: “Tsopano ndadziwadi kuti ndinu munthu wa Mulungu+ ndipo mawu a Yehova amene ali m’kamwa mwanu ndi oona.”+

  • 1 Mafumu 19:16
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 16 Ukadzozenso Yehu+ mdzukulu wa Nimusi+ kuti akhale mfumu ya Isiraeli, ndipo Elisa+ mwana wa Safati wa ku Abele-mehola,+ ukam’dzoze kuti akhale mneneri m’malo mwa iwe.+

  • 2 Mafumu 3:12
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 12 Atamva zimenezo, Yehosafati anati: “Mawu a Yehova ali mwa iye.” Choncho mfumu ya Isiraeli, Yehosafati, ndi mfumu ya Edomu, anapita kwa Elisa.

  • 2 Mafumu 4:9
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 9 Patapita nthawi, mayiyo anauza mwamuna wake+ kuti: “Tsopano ndikudziwa kuti munthu amene amadzera kuno nthawi zonse uja, ndi munthu woyera wa Mulungu.+

  • 2 Mafumu 6:32
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 32 Tsopano Elisa anali atakhala m’nyumba mwake pamodzi ndi akulu+ pamene mfumu inatumiza mthenga kwa iye. Mthengayo asanafike, Elisa anauza akuluwo kuti: “Kodi mwaona kuti mwana wa munthu wopha anthu+ uja watumiza munthu kuti adzandidule mutu? Muonetsetse kuti mthengayo akangofika mutseke chitseko ndipo muchitsamire kuti asathe kulowa. Kodi mapazi a mbuye wake si amene akumveka+ pambuyo pakewo?”

  • 2 Mafumu 8:4
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 4 Pa nthawiyo, mfumu inali ikulankhula ndi Gehazi+ mtumiki wa munthu wa Mulungu woona, kuti: “Ndifotokozere zinthu zonse zazikulu zimene Elisa wachita.”+

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena