Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • 2 Mafumu 2:14
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 14 Ali pamenepo, anatenga chovala chauneneri cha Eliya chimene chinagwa chija n’kumenya nacho madzi a mtsinjewo,+ n’kunena kuti: “Ali kuti Yehova Mulungu wa Eliya?”+ Atamenya madziwo, pang’onopang’ono madziwo anagawanika uku ndi uku, ndipo Elisa anawoloka.

  • 2 Mafumu 2:20
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 20 Elisa atamva zimenezi ananena kuti: “Ndibweretsereni mbale yaing’ono yatsopano yolowa, ndipo muikemo mchere.” Anthuwo anam’bweretseradi mbaleyo.

  • 2 Mafumu 3:17
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 17 chifukwa Yehova wanena kuti: “Anthu inu simuona mphepo kapena mvula, koma chigwa chonsechi chidzaza madzi.+ Inu pamodzi ndi ziweto zanu, ndithu mumwa madziwo.”’+

  • 2 Mafumu 4:4
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 4 Ukakatero, iwe ndi ana akowo mukalowe m’nyumba ndipo mukatseke chitseko. Ndiyeno uzikathira mafutawo m’zotengerazo. Zimene zadzaza uzikaziika pambali.”

  • 2 Mafumu 5:14
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 14 Namani atamva zimenezi, anatsetserekera ku Yorodano n’kukamira maulendo 7, mogwirizana ndi mawu a munthu wa Mulungu woona+ uja. Pambuyo pake, mnofu wake unabwerera mwakale moti unakhala ngati mnofu wa kamnyamata,+ ndipo anakhala woyera.+

  • 2 Mafumu 5:27
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 27 Tsopano khate+ la Namani limamatira iweyo ndi mbadwa zako mpaka kalekale.”*+ Nthawi yomweyo Gehazi anachoka pamaso pa Elisa, atachita khate loyera kuti mbuu.+

  • 2 Mafumu 6:6
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 6 Munthu wa Mulungu woonayo anafunsa kuti: “Yagwera pati?” Iye anamusonyeza pamene inagwera. Nthawi yomweyo Elisa anadula kamtengo n’kukaponya pamalopo ndipo nkhwangwayo inayandama.+

  • 2 Mafumu 7:1
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 7 Tsopano Elisa anati: “Amuna inu, mverani mawu a Yehova.+ Yehova wanena kuti, ‘Mawa chapanthawi ngati ino, pachipata cha Samariya, ufa wosalala wokwana muyezo umodzi wa seya,* mtengo wake udzakhala sekeli* limodzi, ndipo balere wokwana miyezo iwiri ya seya, mtengo wake udzakhalanso sekeli limodzi.’”+

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena