-
2 Mbiri 29:25Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
25 Pa nthawi imeneyi, Hezekiya anaika Alevi+ panyumba ya Yehova atanyamula zinganga,+ zoimbira za zingwe,+ ndi azeze.+ Iwo anali kutsatira ndondomeko yoimbira imene anaikhazikitsa Davide,+ Gadi+ yemwe anali wamasomphenya wa mfumu, ndi mneneri Natani,+ popeza ndondomekoyo inachokera kwa Yehova kudzera mwa aneneri ake.+
-
-
Ezara 3:10Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
10 Tsopano anthu amene anali kugwira ntchito yomanga nyumbayo anamaliza kumanga maziko+ a kachisi wa Yehova. Atatero, ansembe ovala zovala zaunsembe+ omwe ananyamula malipenga,+ ndiponso Alevi ana a Asafu+ omwe ananyamula zinganga,+ anaimirira kuti atamande Yehova motsatira dongosolo+ limene Davide mfumu ya Isiraeli anakhazikitsa.
-