Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • 2 Samueli 16:23
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 23 Ndiyeno masiku amenewo munthu akalandira malangizo kwa Ahitofeli, zinali ngati kuti munthu wafunsira malangizo kwa Mulungu woona. Umu ndi mmene malangizo+ onse a Ahitofeli+ analili, kwa Davide ndi Abisalomu yemwe.

  • Salimo 28:3
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    •  3 Musandikokolole pamodzi ndi anthu oipa komanso anthu amene amachita zopweteka anzawo,+

      Anthu amene amalankhula mawu amtendere ndi anzawo+ koma m’mitima yawo muli zinthu zoipa.+

  • Salimo 57:4
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    •  4 Moyo wanga uli pakati pa mikango.+

      Sindingachitire mwina koma kugona pakati pa ana a anthu, amene ali ngati nyama zoopsa zodya anthu,

      Amene mano awo ali ngati mikondo ndi mivi,+

      Ndipo lilime lawo lili ngati lupanga lakuthwa.+

  • Salimo 59:7
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    •  7 Taonani! Amabwetuka ndi pakamwa pawo.+

      Milomo yawo ili ngati malupanga,+

      Pakuti iwo amati: “Ndani akumvetsera?”+

  • Salimo 62:4
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    •  4 Iwo amapatsa munthu malangizo kuti amukope ndi kumutsitsa pamalo ake aulemu.+

      Bodza limawasangalatsa.+

      Iwo amadalitsa ndi pakamwa pawo, koma mumtima mwawo amatemberera.+ [Seʹlah.]

  • Mateyu 26:25
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 25 Poyankha, Yudasi amene anali atatsala pang’ono kumupereka anati: “Nanga n’kukhala ine Rabi?” Iye anati: “Wanena wekha.”

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena