Yesaya 50:6 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 6 Msana wanga ndinaupereka kwa ondimenya, ndipo masaya anga+ ndinawapereka kwa ozula ndevu. Nkhope yanga sindinaitchinjirize kuti isachitidwe zinthu zamanyazi ndi kulavuliridwa.+ Yesaya 53:3 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 3 Iye ananyozedwa ndipo anthu anali kumupewa.+ Anali munthu amene anadziwa kupweteka ndiponso amene anadziwa matenda.+ Ife tinali kuyang’ana kumbali kuti tisaone nkhope yake.+ Ananyozedwa ndipo tinamuona ngati wopanda pake.+ Mateyu 26:67 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 67 Kenako anayamba kumulavulira kunkhope+ ndi kum’menya+ nkhonya. Ena anamuwomba mbama,+ Mateyu 27:29 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 29 Komanso analuka chisoti chachifumu chaminga ndi kumuveka kumutu n’kumupatsa bango m’dzanja lake lamanja. Kenako anamugwadira ndi kum’chitira zachipongwe+ kuti: “Mtendere ukhale nanu, inu Mfumu ya Ayuda!”+
6 Msana wanga ndinaupereka kwa ondimenya, ndipo masaya anga+ ndinawapereka kwa ozula ndevu. Nkhope yanga sindinaitchinjirize kuti isachitidwe zinthu zamanyazi ndi kulavuliridwa.+
3 Iye ananyozedwa ndipo anthu anali kumupewa.+ Anali munthu amene anadziwa kupweteka ndiponso amene anadziwa matenda.+ Ife tinali kuyang’ana kumbali kuti tisaone nkhope yake.+ Ananyozedwa ndipo tinamuona ngati wopanda pake.+
29 Komanso analuka chisoti chachifumu chaminga ndi kumuveka kumutu n’kumupatsa bango m’dzanja lake lamanja. Kenako anamugwadira ndi kum’chitira zachipongwe+ kuti: “Mtendere ukhale nanu, inu Mfumu ya Ayuda!”+