Salimo 25:9 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 9 Adzachititsa ofatsa kutsatira zigamulo zake,+Ndipo adzaphunzitsa ofatsa kuyenda m’njira yake.+ Salimo 32:8 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 8 Inu munati: “Ndidzakupatsa nzeru ndi kukulangiza njira yoti uyendemo.+Ndidzakupatsa malangizo ndi kukuyang’anira.+ Salimo 37:23 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 23 Yehova walimbitsa mapazi a munthu wamphamvu zake,+Ndipo Mulungu amakondwera ndi njira zake.+ Salimo 143:10 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 10 Ndiphunzitseni kuchita chifuniro chanu,+Pakuti inu ndinu Mulungu wanga.+Mzimu wanu ndi wabwino.+Unditsogolere m’dziko la olungama.+ Miyambo 3:6 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 6 Uzim’kumbukira m’njira zako zonse,+ ndipo iye adzawongola njira zako.+ Yesaya 58:8 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 8 “Mukatero kuwala kwanu kudzaonekera ngati m’bandakucha,+ ndipo mudzachira mofulumira kwambiri.+ Chilungamo chanu chizidzayenda patsogolo panu,+ ndipo ulemerero wa Yehova uzidzalondera kumbuyo kwanu.+
8 Inu munati: “Ndidzakupatsa nzeru ndi kukulangiza njira yoti uyendemo.+Ndidzakupatsa malangizo ndi kukuyang’anira.+
10 Ndiphunzitseni kuchita chifuniro chanu,+Pakuti inu ndinu Mulungu wanga.+Mzimu wanu ndi wabwino.+Unditsogolere m’dziko la olungama.+
8 “Mukatero kuwala kwanu kudzaonekera ngati m’bandakucha,+ ndipo mudzachira mofulumira kwambiri.+ Chilungamo chanu chizidzayenda patsogolo panu,+ ndipo ulemerero wa Yehova uzidzalondera kumbuyo kwanu.+