Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • Ezara 2:1
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 2 Awa ndiwo anali anthu a m’chigawo*+ amene anatuluka mu ukapolo+ wa anthu omwe Nebukadinezara mfumu ya ku Babulo anawatengera+ ku Babulo. Anthuwa anabwerera+ ku Yerusalemu ndi ku Yuda,+ aliyense kumzinda wakwawo.

  • Salimo 14:7
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    •  7 Haa! Zikanakhala bwino m’Ziyoni mukanapezeka chipulumutso cha Isiraeli.+

      Yehova akadzasonkhanitsa ndi kubwezeretsa anthu ake amene anagwidwa ndi kutengedwa kupita kudziko lina,+

      Yakobo adzasangalale, Isiraeli adzakondwere.+

  • Salimo 53:6
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    •  6 Haa! Zikanakhala bwino m’Ziyoni mukanapezeka chipulumutso cha Isiraeli.+

      Yehova akadzasonkhanitsa ndi kubwezeretsa anthu ake amene agwidwa ndi kutengedwa kupita kudziko lina,+

      Yakobo adzasangalale, Isiraeli adzakondwere.+

  • Yeremiya 30:18
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 18 Yehova wanena kuti: “Ndikusonkhanitsa anthu a m’mahema a Yakobo+ amene anagwidwa ndi kutengedwa kupita kudziko lina ndipo ndidzamvera chisoni malo okhala a Yakobo. Mzinda udzamangidwanso pachiunda chake+ ndipo nsanja yokhalamo idzakhala pamalo ake oyenera.+

  • Yeremiya 31:23
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 23 Yehova wa makamu, Mulungu wa Isiraeli, wanena kuti: “Ndikadzasonkhanitsa anthu a mtundu wawo amene anagwidwa ndi kutengedwa kupita kudziko lina, iwo adzanena mawu awa m’dziko la Yuda ndi m’mizinda yake kuti, ‘Yehova akudalitse iwe+ malo olungama okhalamo,+ iwe phiri lopatulika.’+

  • Ezekieli 39:25
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 25 “Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa, wanena kuti, ‘Tsopano ndibweretsa ana a Yakobo omwe anatengedwa kupita kumayiko ena,+ ndipo ndichitira chifundo nyumba yonse ya Isiraeli.+ Nditeteza dzina langa loyera kuti lisadetsedwe.*+

  • Yoweli 3:1
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 3 “Ndiyeno masiku amenewo ndiponso pa nthawi imeneyo,+ ndidzabwezeretsa anthu a ku Yuda ndi a ku Yerusalemu amene anagwidwa ukapolo.+

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena