Salimo 5:9 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 9 Pakuti m’kamwa mwawo simutuluka mawu okhulupirika.+Mitima yawo yadzaza ndi zinthu zoipa.+Mmero wawo ndi manda otseguka.+Iwo amalankhula ndi lilime lachinyengo.+ Salimo 28:3 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 3 Musandikokolole pamodzi ndi anthu oipa komanso anthu amene amachita zopweteka anzawo,+Anthu amene amalankhula mawu amtendere ndi anzawo+ koma m’mitima yawo muli zinthu zoipa.+ Salimo 62:4 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 4 Iwo amapatsa munthu malangizo kuti amukope ndi kumutsitsa pamalo ake aulemu.+Bodza limawasangalatsa.+Iwo amadalitsa ndi pakamwa pawo, koma mumtima mwawo amatemberera.+ [Seʹlah.] Yeremiya 9:8 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 8 Lilime lawo ndiwo muvi wophera anthu.+ Limalankhula chinyengo chokhachokha. Munthu aliyense amalankhula mwamtendere ndi mnzake, koma mumtima mwake amakonza chiwembu.”+ Aroma 16:18 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 18 Pakuti anthu oterowo si akapolo a Ambuye wathu Khristu, koma a mimba zawo.+ Ndipo mwa kulankhula mawu okopa+ ndi achinyengo+ amanyenga anthu oona mtima.
9 Pakuti m’kamwa mwawo simutuluka mawu okhulupirika.+Mitima yawo yadzaza ndi zinthu zoipa.+Mmero wawo ndi manda otseguka.+Iwo amalankhula ndi lilime lachinyengo.+
3 Musandikokolole pamodzi ndi anthu oipa komanso anthu amene amachita zopweteka anzawo,+Anthu amene amalankhula mawu amtendere ndi anzawo+ koma m’mitima yawo muli zinthu zoipa.+
4 Iwo amapatsa munthu malangizo kuti amukope ndi kumutsitsa pamalo ake aulemu.+Bodza limawasangalatsa.+Iwo amadalitsa ndi pakamwa pawo, koma mumtima mwawo amatemberera.+ [Seʹlah.]
8 Lilime lawo ndiwo muvi wophera anthu.+ Limalankhula chinyengo chokhachokha. Munthu aliyense amalankhula mwamtendere ndi mnzake, koma mumtima mwake amakonza chiwembu.”+
18 Pakuti anthu oterowo si akapolo a Ambuye wathu Khristu, koma a mimba zawo.+ Ndipo mwa kulankhula mawu okopa+ ndi achinyengo+ amanyenga anthu oona mtima.