Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • Oweruza 3:9
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 9 Ndipo ana a Isiraeli anayamba kufuulira Yehova kuti awathandize.+ Pamenepo Yehova anapereka mpulumutsi+ wa ana a Isiraeli kuti awapulumutse. Ameneyu anali Otiniyeli,+ mwana wamwamuna wa Kenazi,+ mng’ono wake wa Kalebe.+

  • Oweruza 4:3
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 3 Ana a Isiraeli anayamba kulirira Yehova,+ chifukwa Yabini anawapondereza+ kwambiri zaka 20, ndipo iye anali ndi magaleta ankhondo 900 okhala ndi zitsulo zazitali zakuthwa m’mawilo.+

  • Oweruza 10:15
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 15 Poyankha, ana a Isiraeli anauza Yehova kuti: “Tachimwa.+ Inuyo mutichite zilizonse zimene zingakukomereni m’maso mwanu.+ Koma chonde, ingotipulumutsani lero.”+

  • 1 Samueli 7:8
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 8 Chotero ana a Isiraeli anauza Samueli kuti: “Usakhale chete, koma utipempherere kwa Yehova Mulungu kuti atithandize,+ kuti atipulumutse m’manja mwa Afilisiti.”

  • Nehemiya 9:28
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 28 “Koma akangokhala pa mtendere, anali kuchitanso zoipa pamaso panu+ ndipo munali kuwasiya m’manja mwa adani awo amene anali kuwapondaponda.+ Zikatero, anali kubweranso kwa inu ndi kupempha thandizo lanu,+ ndipo inu munali kumva muli kumwambako+ ndi kuwapulumutsa mobwerezabwereza, chifukwa cha chifundo chanu chachikulu.+

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena