Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • Ekisodo 7:20
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 20 Nthawi yomweyo Mose ndi Aroni anachita zomwezo,+ monga momwe Yehova anawalamulira.+ Ndipo Aroni anatenga ndodo yake ndi kumenya madzi a mumtsinje wa Nailo, Farao ndi atumiki ake akuona.+ Pamenepo madzi onse a mumtsinje wa Nailo anasanduka magazi.+

  • Ekisodo 8:6
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 6 Pamenepo Aroni anatambasula dzanja lake ndi kuloza madzi onse a mu Iguputo, ndipo achule anayamba kutuluka ndi kudzaza dziko lonse la Iguputo.

  • Ekisodo 8:17
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 17 Iwo anachitadi zomwezo. Choncho Aroni anatambasula dzanja lake ndi kumenya fumbi lapansi ndi ndodo yake, ndipo ntchentchezo zinayamba kuluma anthu ndi nyama zomwe. Fumbi lonse la m’dziko la Iguputo linasanduka ntchentche zoluma.+

  • Ekisodo 9:6
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 6 Mogwirizana ndi mawu ake, Yehova anachitadi zimenezi tsiku lotsatira, ndipo ziweto zamitundu yonse za Aiguputo zinayamba kufa,+ koma palibe chiweto ngakhale chimodzi cha ana a Isiraeli chimene chinafa.

  • Ekisodo 9:10
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 10 Choncho iwo anatenga mwaye wa mu uvuni ndi kuima pamaso pa Farao. Pamenepo Mose anauponya m’mwamba, ndipo unayambitsa zithupsa zomaphulika,+ pa anthu ndi nyama.

  • Ekisodo 9:23
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 23 Ndipo Mose anatambasula dzanja lake ndi kuloza kumwamba ndi ndodo yake. Atatero, Yehova anachititsa mabingu ndipo anagwetsa matalala+ ndi moto padziko lapansi. Choncho Yehova anapitiriza kugwetsa matalala padziko la Iguputo.

  • Ekisodo 10:12
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 12 Chotero Yehova anauza Mose kuti: “Tambasula+ dzanja lako ndi kuloza dziko la Iguputo, kuti dzombe ligwe m’dziko lonselo ndi kudya zomera zonse za m’dzikomo, chilichonse chimene matalala anasiya.”+

  • Ekisodo 10:21
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 21 Pamenepo Yehova anauza Mose kuti: “Tambasula dzanja lako ndi kuloza kumwamba+ kuti m’dziko lonse la Iguputo mugwe mdima wandiweyani.”

  • Deuteronomo 4:34
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 34 Kapena kodi Mulungu anayamba wapitapo kukadzitengera mtundu wa anthu pakati pa mtundu wina ndi mayesero,+ zizindikiro,+ zozizwitsa,+ nkhondo,+ dzanja lamphamvu,+ mkono wotambasula,+ ndi zoopsa zazikulu+ zofanana ndi zimene Yehova Mulungu wanu anakuchitirani ku Iguputo inu mukuona?

  • Nehemiya 9:10
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 10 Ndiyeno munaonetsa Farao zizindikiro ndi zozizwitsa zomukhaulitsa pamodzi ndi atumiki ake onse ndi anthu onse okhala m’dziko lake.+ Munatero chifukwa munadziwa kuti iwo anachita zinthu modzikuza+ kwa makolo athu. Pamenepo munadzipangira dzina+ kufikira lero.

  • Salimo 105:27
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 27 Iwowa anasonyeza Aiguputo zizindikiro za Mulungu,+

      Ndi zozizwitsa m’dziko la Hamu.+

  • Machitidwe 7:36
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 36 Munthu ameneyo anawatsogolera ndi kutuluka nawo,+ atachita zodabwitsa ndi zizindikiro mu Iguputo,+ pa Nyanja Yofiira+ ndi m’chipululu kwa zaka 40.+

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena