Masalimo
Salimo la Davide. Masikili.*
32 Wodala ndi munthu amene wakhululukidwa zolakwa zake, amene machimo ake aphimbidwa.+
3 Pamene ndinakhala chete osaulula machimo anga, mafupa anga anafooka, chifukwa tsiku lonse ndinali kuvutika mumtima mwanga.+
4 Pakuti dzanja lanu linali kundilemera usana ndi usiku.+
Mphamvu zanga zinauma ngati madzi m’nyengo yotentha ya chilimwe.+ [Seʹlah.]
5 Pamapeto pake ndinaulula tchimo langa kwa inu, ndipo sindinabise cholakwa changa.+
Ndinati: “Ndidzaulula kwa Yehova machimo anga.”+
Ndipo inu munandikhululukira zolakwa zanga ndi machimo anga.+ [Seʹlah.]
6 Pa chifukwa chimenechi, aliyense wokhulupirika adzapemphera kwa inu,+
Pa nthawi imene inu mungapezeke.+
Ndipo madzi ambiri osefukira sadzamukhudza ngakhale pang’ono.+
7 Ndinu malo anga obisalamo, mudzanditeteza ku masautso.+
Mudzachititsa kuti chisangalalo chindizungulire pamene mukundipulumutsa.+ [Seʹlah.]
8 Inu munati: “Ndidzakupatsa nzeru ndi kukulangiza njira yoti uyendemo.+
Ndidzakupatsa malangizo ndi kukuyang’anira.+
9 Anthu inu, musakhale ngati hatchi kapena nyulu* yosazindikira,+
Imene munthu amachita kuimanga chingwe chapakamwa ndi chapamutu kuti athetse kupulupudza kwake,+
Ndi kuti aiyandikire.”+