Genesis 20:6 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 6 Pamenepo Mulungu woona anamuuza m’malotomo kuti: “Inenso ndinadziwa kuti mtima wako sunakutsutse pochita zimenezi,+ ndipo ndinakutchinga kuti usandichimwire.+ Ndiye chifukwa chake sindinakulole kuti umukhudze mkaziyu.+ Deuteronomo 17:12 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 12 Munthu amene adzadzikuza mwa kusamvera wansembe amene akutumikira Yehova Mulungu wako kapena mwa kusamvera woweruza,+ munthu ameneyo afe ndithu.+ Muzichotsa woipayo mu Isiraeli.+ 1 Samueli 15:23 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 23 Pakuti kupanduka+ n’chimodzimodzi ndi tchimo la kuwombeza,+ ndipo kuchita zinthu modzikuza n’chimodzimodzi ndi kugwiritsa ntchito mphamvu zamatsenga ndiponso aterafi.+ Popeza iwe wakana mawu a Yehova,+ iyenso wakukana kuti usakhalenso mfumu.”+ 2 Samueli 6:7 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 7 Pamenepo mkwiyo wa Yehova+ unayakira Uza ndipo Mulungu woona anamukantha+ pomwepo chifukwa cha kuchita chinthu chosalemekeza Mulungu chimenechi. Moti Uza anafera pomwepo, pafupi ndi likasa la Mulungu woona.+ 2 Mbiri 26:16 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 16 Koma atangokhala wamphamvu, mtima wake unadzikuza+ mpaka kufika pom’pweteketsa.+ Choncho anachita zosakhulupirika kwa Yehova Mulungu wake ndipo anapita m’kachisi wa Yehova kukafukiza paguwa lansembe zofukiza.+
6 Pamenepo Mulungu woona anamuuza m’malotomo kuti: “Inenso ndinadziwa kuti mtima wako sunakutsutse pochita zimenezi,+ ndipo ndinakutchinga kuti usandichimwire.+ Ndiye chifukwa chake sindinakulole kuti umukhudze mkaziyu.+
12 Munthu amene adzadzikuza mwa kusamvera wansembe amene akutumikira Yehova Mulungu wako kapena mwa kusamvera woweruza,+ munthu ameneyo afe ndithu.+ Muzichotsa woipayo mu Isiraeli.+
23 Pakuti kupanduka+ n’chimodzimodzi ndi tchimo la kuwombeza,+ ndipo kuchita zinthu modzikuza n’chimodzimodzi ndi kugwiritsa ntchito mphamvu zamatsenga ndiponso aterafi.+ Popeza iwe wakana mawu a Yehova,+ iyenso wakukana kuti usakhalenso mfumu.”+
7 Pamenepo mkwiyo wa Yehova+ unayakira Uza ndipo Mulungu woona anamukantha+ pomwepo chifukwa cha kuchita chinthu chosalemekeza Mulungu chimenechi. Moti Uza anafera pomwepo, pafupi ndi likasa la Mulungu woona.+
16 Koma atangokhala wamphamvu, mtima wake unadzikuza+ mpaka kufika pom’pweteketsa.+ Choncho anachita zosakhulupirika kwa Yehova Mulungu wake ndipo anapita m’kachisi wa Yehova kukafukiza paguwa lansembe zofukiza.+