Levitiko 20:9 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 9 “‘Munthu akatemberera bambo ndi mayi ake,+ aziphedwa ndithu.+ Iye watemberera bambo ndi mayi ake. Mlandu wa magazi ake ukhale wa iye mwini.+ Deuteronomo 27:16 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 16 “‘Wotembereredwa ndi munthu wonyoza bambo ake kapena mayi ake.’+ (Anthu onse ayankhe kuti, ‘Zikhale momwemo!’) Miyambo 17:25 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 25 Mwana wopusa amakhumudwitsa bambo ake,+ ndipo amamvetsa chisoni mayi ake amene anam’bereka.+ Miyambo 20:20 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 20 Aliyense wotemberera bambo ake ndi mayi ake,+ nyale yake idzazimitsidwa kukagwa mdima.+ Miyambo 23:22 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 22 Mvera bambo ako amene anakubereka,+ ndipo usanyoze mayi ako chifukwa chakuti akalamba.+ Miyambo 30:11 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 11 Pali m’badwo umene umatemberera ngakhale abambo awo ndiponso umene sudalitsa ngakhale amayi awo.+ Miyambo 30:17 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 17 Diso limene limanyoza bambo ake ndiponso limene silimvera mayi ake,+ akhwangwala a kuchigwa* adzalikolowola ndipo ana a chiwombankhanga adzalidya. Mika 7:6 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 6 Pakuti mwana wamwamuna akunyoza bambo ake. Mwana wamkazi akuukira mayi ake+ ndipo mkazi wokwatiwa akuukira apongozi ake aakazi.+ Adani ake a munthu ndi anthu a m’banja lake.+ 2 Timoteyo 3:2 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 2 Pakuti anthu adzakhala odzikonda, okonda ndalama, odzimva, odzikweza, onyoza, osamvera makolo,+ osayamika, osakhulupirika,+
9 “‘Munthu akatemberera bambo ndi mayi ake,+ aziphedwa ndithu.+ Iye watemberera bambo ndi mayi ake. Mlandu wa magazi ake ukhale wa iye mwini.+
16 “‘Wotembereredwa ndi munthu wonyoza bambo ake kapena mayi ake.’+ (Anthu onse ayankhe kuti, ‘Zikhale momwemo!’)
17 Diso limene limanyoza bambo ake ndiponso limene silimvera mayi ake,+ akhwangwala a kuchigwa* adzalikolowola ndipo ana a chiwombankhanga adzalidya.
6 Pakuti mwana wamwamuna akunyoza bambo ake. Mwana wamkazi akuukira mayi ake+ ndipo mkazi wokwatiwa akuukira apongozi ake aakazi.+ Adani ake a munthu ndi anthu a m’banja lake.+
2 Pakuti anthu adzakhala odzikonda, okonda ndalama, odzimva, odzikweza, onyoza, osamvera makolo,+ osayamika, osakhulupirika,+