Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • Ekisodo 7:22
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 22 Komano, ansembe ochita zamatsenga a ku Iguputo anachitanso zomwezo mwa matsenga awo,+ moti Farao anaumitsabe mtima wake,+ ndipo sanamvere Mose ndi Aroni, monga Yehova ananenera.+

  • Nehemiya 9:29
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 29 Ngakhale kuti munali kuwalimbikitsa+ kuti abwerere ku chilamulo chanu,+ iwo anali kuchita zinthu modzikuza+ ndipo sanali kumva malamulo anu. Anachimwira zigamulo zanu,+ zimene ngati munthu azitsatira adzakhala ndi moyo chifukwa cha zigamulozo.+ Iwo anatseka makutu*+ awo ndi kuumitsa khosi+ lawo ndipo sanamvere.+

  • Yobu 9:4
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    •  4 Iye ali ndi mtima wanzeru ndiponso mphamvu zambiri.+

      Ndani angachite naye makani,* koma osavulala?+

  • Miyambo 29:1
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 29 Munthu wodzudzulidwa kawirikawiri+ koma amene amaumitsa khosi lake,+ adzathyoledwa mwadzidzidzi ndipo akadzatero sadzachira.+

  • Yesaya 30:1
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 30 Yehova wanena kuti: “Tsoka kwa ana aamuna osamva,+ amene amakonda kuchita zofuna zawo osati zofuna zanga,+ amene amapanga mgwirizano mwa kuthira pansi chakumwa monga nsembe motsutsana ndi zofuna zanga,* kuti awonjezere tchimo pa tchimo,+

  • Yeremiya 16:12
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 12 Ndipo inu mwachita zinthu zoipa kwambiri kuposa makolo anu.+ Aliyense wa inu akupitiriza kuumitsa mtima+ wake woipawo ndipo simukundimvera.+

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena