Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • Deuteronomo 29:19
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 19 “Ndiyeno zikachitika kuti wina amene wamva mawu a lumbiro+ ili, walankhula modzitama mumtima mwake kuti, ‘Ndidzakhala ndi mtendere+ ngakhale kuti ndidzayenda motsatira zofuna za mtima wanga,’+ koma ali ndi cholinga chowononga wina aliyense, mofanana ndi kukokolola mtengo wothiriridwa bwino ndi wosathiriridwa womwe,

  • Oweruza 2:19
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 19 Ndiyeno zinali kuchitika kuti woweruza akamwalira, ana a Isiraeli anali kupatuka ndi kuchita zinthu zowawonongetsa kuposanso makolo awo. Anali kuchita zimenezi mwa kutsatira milungu ina, kuitumikira ndi kuigwadira.+ Iwo sanasiye zochita zawozo ndiponso khalidwe lawo la unkhutukumve.+

  • Nehemiya 9:29
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 29 Ngakhale kuti munali kuwalimbikitsa+ kuti abwerere ku chilamulo chanu,+ iwo anali kuchita zinthu modzikuza+ ndipo sanali kumva malamulo anu. Anachimwira zigamulo zanu,+ zimene ngati munthu azitsatira adzakhala ndi moyo chifukwa cha zigamulozo.+ Iwo anatseka makutu*+ awo ndi kuumitsa khosi+ lawo ndipo sanamvere.+

  • Yeremiya 6:28
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 28 Onse ndi anthu ouma khosi kwambiri,+ oyenda uku ndi uku ngati anthu amiseche.+ Iwo ali ngati mkuwa ndi chitsulo. Onsewo ndi anthu owononga.+

  • Yeremiya 7:24
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 24 Koma iwo sanamvere kapena kutchera khutu,+ ndipo anapitiriza kuyenda mwa zofuna zawo, mwa kuuma kwa mtima wawo woipawo,+ mwakuti anali kuyenda mobwerera m’mbuyo osati mopita patsogolo,+

  • Yeremiya 9:14
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 14 koma iwo anapitirizabe kuumitsa mitima yawo+ ndi kutsatira mafano a Baala,+ zinthu zimene anaphunzitsidwa ndi makolo awo.+

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena