Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • Nehemiya 9:29
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 29 Ngakhale kuti munali kuwalimbikitsa+ kuti abwerere ku chilamulo chanu,+ iwo anali kuchita zinthu modzikuza+ ndipo sanali kumva malamulo anu. Anachimwira zigamulo zanu,+ zimene ngati munthu azitsatira adzakhala ndi moyo chifukwa cha zigamulozo.+ Iwo anatseka makutu*+ awo ndi kuumitsa khosi+ lawo ndipo sanamvere.+

  • Miyambo 28:14
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 14 Wodala ndi munthu amene amaopa Mulungu nthawi zonse,+ koma woumitsa mtima wake adzagwera m’tsoka.+

  • Yesaya 30:1
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 30 Yehova wanena kuti: “Tsoka kwa ana aamuna osamva,+ amene amakonda kuchita zofuna zawo osati zofuna zanga,+ amene amapanga mgwirizano mwa kuthira pansi chakumwa monga nsembe motsutsana ndi zofuna zanga,* kuti awonjezere tchimo pa tchimo,+

  • Yeremiya 3:17
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 17 Pa nthawiyo mzinda wa Yerusalemu adzautcha kuti mpando wachifumu wa Yehova.+ Ndipo mitundu yonse adzaisonkhanitsira+ ku Yerusalemu kuti ikatamande dzina la Yehova+ kumeneko. Iwo sadzaumitsanso mitima yawo yoipayo.”+

  • Yeremiya 6:28
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 28 Onse ndi anthu ouma khosi kwambiri,+ oyenda uku ndi uku ngati anthu amiseche.+ Iwo ali ngati mkuwa ndi chitsulo. Onsewo ndi anthu owononga.+

  • Zekariya 7:12
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 12 Iwo anaumitsa mtima wawo+ ngati mwala wolimba kwambiri kuti asamvere malamulo+ ndi mawu a Yehova wa makamu, amene anawatumizira mwa mzimu wake+ kudzera mwa aneneri akale.+ Choncho Yehova wa makamu anakwiya kwambiri.”+

  • Aroma 1:21
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 21 Chifukwa chakuti, ngakhale anam’dziwa Mulungu, iwo sanam’patse ulemerero monga Mulungu kapena kumuyamikira.+ M’malomwake anayamba kulingalira zinthu zopanda pake+ ndipo mtima wawo wopusawo unachita mdima.+

  • Aroma 2:5
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 5 Koma chifukwa chakuti ndiwe wosafuna kusintha khalidwe+ ndiponso wa mtima wosalapa,+ ukudzisungira mkwiyo wa Mulungu.+ Mulungu adzasonyeza mkwiyo+ umenewu pa tsiku loulula+ chiweruzo chake cholungama.+

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena