-
Yeremiya 16:19Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
19 Inu Yehova, ndinu mphamvu yanga, malo anga achitetezo ndi malo anga othawirako pa tsiku la tsoka.+ Mitundu ya anthu idzabwera kwa inu kuchokera kumalekezero a dziko lapansi,+ ndipo idzati: “Ndithudi makolo athu analandira mafano* monga cholowa chawo.+ Analandira zinthu zachabechabe ndi zinthu zosapindulitsa.”+
-
-
Yeremiya 44:17Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
17 Ife tichita zonse zimene tanena.+ Tipereka nsembe zautsi ndi kuthira nsembe zachakumwa+ kwa ‘mfumukazi yakumwamba.’+ Tichita zimenezi monga mmene ife,+ makolo athu,+ mafumu athu+ ndi akalonga athu anachitira m’mizinda ya Yuda ndi m’misewu ya Yerusalemu pamene tinali kudya mkate ndi kukhuta ndipo zinthu zinali kutiyendera bwino, moti sitinaone tsoka lililonse.+
-