-
Yoswa 7:21Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
21 Nditaona+ chovala chamtengo wapatali cha ku Sinara,+ pakati pa katundu wotsalayo, chokongola m’maonekedwe, komanso masekeli* a siliva 200, ndi mtanda umodzi wa golide wolemera masekeli 50, ndinazikhumba zinthuzo,+ ndipo ndinazitenga.+ Panopo chovalacho ndinachikumbira pansi, pakati pa hema wanga, pamodzi ndi ndalamazo, ndipo ndalamazo zili pansi pa chovalacho.”+
-
-
Ezekieli 8:17Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
17 Iye anapitiriza kundiuza kuti: “Iwe mwana wa munthu, kodi waona zimenezi? Kodi a nyumba ya Yuda akuona ngati ndi chinthu chaching’ono kuchita zinthu zonyansa zimene akuchita panozi? Kodi akufunanso kuti adzaze dzikoli ndi chiwawa+ n’kundikwiyitsa kachiwiri? Kodi waonanso kuti iwowo akulozetsa nthambi* kumphuno kwanga?
-