Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • Genesis 41:44
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 44 Farao anauzanso Yosefe kuti: “Farao ndine, koma popanda chilolezo chako, palibe wina aliyense angachite* kanthu m’dziko lonse la Iguputo.”+

  • 1 Mafumu 2:25
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 25 Nthawi yomweyo Mfumu Solomo inatumiza lamulo kudzera mwa Benaya+ mwana wa Yehoyada. Iye anapita kukakantha Adoniya, n’kumupha.+

  • Ezara 7:26
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 26 Aliyense wosatsatira chilamulo cha Mulungu wako+ ndi chilamulo cha mfumu, azipatsidwa chiweruzo msangamsanga, kaya choti aphedwe,+ athamangitsidwe,+ alipitsidwe ndalama,+ kapena aikidwe m’ndende.”

  • Danieli 3:15
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 15 Tsopano ngati mwakonzeka kuti mukamva kulira kwa lipenga, chitoliro, zeze wamng’ono, zoimbira zosiyanasiyana za zingwe, chitoliro chathumba ndi zipangizo zosiyanasiyana zoimbira,+ mugwada n’kuwerama mpaka nkhope zanu pansi ndi kulambira fano lagolide, zili bwino. Koma ngati simulilambira, nthawi yomweyo muponyedwa m’ng’anjo yoyaka moto. Ndipo ndi mulungu uti amene angakupulumutseni m’manja mwanga?”+

  • Aroma 13:1
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 13 Munthu aliyense azimvera+ olamulira akuluakulu,+ chifukwa palibe ulamuliro+ umene ungakhalepo kupatulapo ngati Mulungu waulola.+ Olamulira amene alipowa ali m’malo awo osiyanasiyana+ mololedwa ndi Mulungu.+

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena